Pamene mitengo ya zinthu ikupitilira kukwera monga mafuta galimoto,ophikira zakudya,magetsi ndi zina zotero nalo bungwe logawa madzi lati malingana ndikukwera kwa zinthu bungweli likulephera kupanga zinthu zina zomwe zingathe kupititsa patsogolo ntchito yogawa madzi mdziko muno.
Malingana ndi chikalata chomwe Avant publications yaona chikusonyeza kuti Bungwe logawa madzi muchigawo chakumwera lakweza mtengo ndi 50%, Blantyre waterboard yakweza ndi 40% , central region waterboard yakweza ndi 65% ndipo Lilongwe waterboard ndi mzuzu waterboard sanalengeze kaye mitengo yawo yatsopano.
Titalankhula ndi azimayi omwe amatunga madzi pa kiyosaki ku bangwe mzinda wa Blantyre ndipo ati “ndizomvesa chisoni kuti tsiku ndi tsiku zinthu zikukwera mtengo ndipo tsopano tisowa mtengo wogwira, enafe timadalira kuti ndi k50 titunga madzi koma kukupitaku tikukaika ngati zitheke.”
Nako ku Salima mzibambo mmodzi yemwe tinalankhula naye wati ” ngati ma bilu amativuta pakale paja nde pano 65% tikwanitsa? Ndipo water board uwauze anyamata awo opereka ma bilu osamaonjezere dala mitengo podinda ma bilu.” Anatero mkuluyi.
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*