KODI ADINDO AKUCHITAPO CHIYANI?

Pali nkhani zina kuzikamba umachita kuopa popeza adindo anasekereza kale ndi malamulo pogwilitsa ntchito mawu a muchizungu oti the matter is in court mawuwa mukawamvetsera bwino amakhala mathero ankhani zambiri zomwe zimayenera kukambidwa.

Nkhani tikukamba pano ndi nkhani yokhuza ma judge komanso apolice. Onse ophwanya malamulo amayenera akumane ndi nthambi ziwirizi ndipo awiriwa amagwira ntchito mothandizana. Koma mwanthawi zonse amayamba ndi apolisi kugwira ntchito omwe amapatsira ma jaji. Ma judge sangagwire munthu paokha ndipo amadalira apolisi, nawo apolisi sangapereke chigamulo amadalira ma judge. Koma pena zimapezeka kuti nthambi ziwirizi zikumakhulana zokhazokha, popeza ena milandu yoyenera chilango ma jaji akumangowataya anthu ndipo anthu ena oyenera kumangidwa apolisi Sakuwamanga.

Pali nkhani zina zomwe zinalowa ku khoti kale kale mpaka pano sizikutha. Mwachisanzo avant publications yapeza kuti milandu yambiri ku khoti ikungounjikika ndipo sikutha, monga milandu ya achisale pano zaka ziwiri zikutha chigamulo sichikuoneka, kodi ma umboni akusowa kapena zikuvuta pati kwenikweni kuti agamulidwe? Anthu omwe anaotcha office ya UTM ndi kupha makolo ndi ana ku Lilongwe pano akuyenda mwa ufulu pa belo. Koma mukuwaganizira bwanji ana kapena achibale a anthuwo? Zikuvuta pati kumaliza nkhaniyi? Naye jomo anachitira nkhaza komanso kugulitsa samusa wa 45,000 komanso nkhuku 35,000. Kumenya anthu ku mademo milandu yake ili ku khoti pano ndi mfulu nkhayi ndikhulupira ilibenso umboni. Nduna za boma zina zinaba ndalama za covid 19 a ACB anatulutsa report koma kuli zii palibe chikuchitika. A Peter mthalika, ndi a mtaba anatchulidwa mu khoti kuti ndiwo amatuma anthu kuti aphe ma albino koma koma sitinamve ma judge akuitanitsa anthuwa kuti akawafunse koma anthu ongotumidwawo anagamulidwa ndipo akuzudzika kamba ka anthu ena omwe ndi afulu pano.

Nkhanizitu ndi zoti zili mmanja mwa ma judge. Izi sizikufunikanso apolisi ayi. Mkulu wa ma judge mzikanda anapereka matsiku 90 kuti nkhanizi zithe kodi zolinga za a mzikamanda zikwanilitsidwa? Ma judge amaliza milandu yonseyi? Nthawitu ikutha.

Tikalowera ku polisi pali zinthu zambiri zomwe nthambiyi sikuchita mokwanira kamba koti oyenera kumangidwa sakumangidwa koma ongoganizilidwa akukalowa.

Posachedwapa pachitika nkhani yomwe ana akumalawi kuno amazuzudwa ndi mu China Lu ke kapena kuti SUSU powajambula makanema onyozetsa munthu wakuda, kuwamenya, kuwajombetsa ku school. Nkhaniyi yaululika ndi mtolankhani wa kunja koma apolisi sakuchitapo kalikonse,

A kaliyopa nawo anabera achinyamata ndalama zochuluka powanamiza ntchito ku polisi kapena tinene kuti uku kunali kuberanso polisi imene, koma apolisi anthu sanagwirebe mkuluyi ati akuwasowa.

Matse anamwalira ndipo boma linapempha kuti apolisi atiuze chomwe chinachitika pofufuza za imfa yake koma mpaka pano kuli zii.

Nkhanizi ndi zambiri koma zikakhala za anthu oziwika zikuthera pofufuza koma anthu wamba nde zaka khumbi akugwira ukaidi wa kalavula gaga komanso olo ube nkhuku kulibe belo.

Apolisi ndi ma judge anthu timakunyadirani gwirani ntchito yanu mwa ukadaulo ndipo awonetseni amalawi kuti ndinu akaswiri. Musachite kudikira president kulamula kuti nkhani ziyende mwa changu.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *