K 2000 YALOWETSA MUNTHU M’MANDA .

Apolisi ku Mponera m’boma la Dowa amanga Dennis Diveliyasi wadzaka 25 kamba kopha bambo mzake chifukwa cha ngongole ya K 2000.Mneneri wa apolisi m’bomali , MacPatson Msadala wati bambo Kamkwamba Jaziyere anatenga nyama ya 1 KG pa mtengo wa K 2000 chaka chathachi kwa Diveliyasi ndipo kufikila pano anali asanapereke.Awiriwa atakumana malo omwera mowa lero, Diveloyasi anayamba kukumbutsa ndalama kwa Kamkwamba yemwe anati sangaperekeso chifukwa ngongoleyo idatha mphamvu.Izi zinakwiyitsa mamuna wadzaka 25yu yemwe anayamba kumenya bambo wadzaka 35yu mpaka kumuvulaza.Kutsatila ndikuvulala kwakukulu pa ndewuyo, anthu anatengera Jaziyere ku chipatala cha Mponera komwe anakamwalira atangofika.Apolisi anapeza Diveliyasi yemwe amumanga ndipo padakali pano ali nchitokosi ku polisi ya Mponera.Bamboyu amachokera mmudzi mwa Kadewere mfumu yaikulu Chakhanza m’boma la Dowa.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *