Mzika ya mdziko la Zimbabwe, Tinashe Sharen, ya zaka 28 zakubadwa, yapeleka chindapusa cha K1 million podzetsa imfa komanso kuyendetsa galimoto mosasamala.
Oimila boma pa mulanduwu, Sub Inspector Danford Otala wa polisi ya Chikwawa anauza bwalo la Chikwawa Magistrate kuti galimoto lomwe Sharen ankayendetsa lidagunda ndi kupha wa njinga ya kapalasa, Alexander Masina wa zaka 11.
Galimotoli lidali la mtundu wa Toyota Hilux, nambala yake AFN 0396 ndipo ngoziyi idachitikira pa mzikiti wa Kasinthula omwe uli m’mudzi mwa Salumeji, mfumu yaikulu Katunga m’bomali.
Nkhaniyi ikuti m’nyamatayu ankaphunzira pa sukulu ya pulaimale ya Namalindi ndipo Sharen ankathamangitsa galimoto modetsa nkhawa.
Sharen adavomera milandu yonse iwiri ndipo Otala adauza bwalo kuti mkuluyu amafunika chilango chokhwima potengera kuti achibale sapeza chipukuta misonzi chilichonse poti galimotoli lidalibe insurance.
Komabe, mzika ya ku Zimbabwe-yi idapempha chifundo cha bwalo ponena kuti kanali koyamba kupalamula, adathandiza pa maliro a m’nyamatayu ndi ndalama komanso ali ndi banja lomwe amalisamalira.
Ndipo First Grade Magistrate Jolam Zebron anagwirizana ndi mbali ya boma nkulamula Sharen kuti alipire K500 000 ngati chindapusa podzetsa imfa komanso K500 000 ina poyendetsa galimoto yopanda insurance.