Bungwe la ACB lati silinatchule maina mu report lomwe linapita kwa a president, lomwe a Chakwera anatchula anthu anayi omwe ena mwa iwo ndi a kaponda mgaga, mkulu wa apolisi komanso wachiwiri kwa msogoleri wa dziko lino.
Malingana ndi mneneri wa ACB a Egritta mdala ati iwo sanamalize kupanga kafukufuku wawo pa za lipoti lokhuza za katangale makamaka pa nkhani ya sattar, choncho iwo sangangatchula mainawa. Tikanakhala kuti tinamaliza kafukufufu bwezi titawatengera anthuwa ku bwalo la milandu. Watero meneneri wa ACB.
Nkhaniyi yadabwitsa anthu kuti ngati ACB sinatchule mainawa a president anawatenga kutiko? Anaikamo okha mainawa mu lipotili? Kodi ngati ACB sinamalize kafukufuku kodi ndichifukwa chani a George kainja anamangidwa mkutulukaso pa Bello tsiku lake lomwero? Kapena mulandu wake siunali umenewu?
Kodi pakati pa ACB ndi a president akunena zoona ndani?
Pano miyezi itatu yatha achakwera atayimitsa anthu anayiwa omwe anatchulidwa mu lipotiyi kuphatikizapo wachiwiri wawo kugwira ntchito za boma zomwe anthu ambiri akuti ndi ndale chabe.
Amalawi ali tcheru tsopano kuti amve kuchokera ku boma kuti cheni ndi chiti poti bungwe lothana ndi katangale lawasambira mmanja a president.
www.avantmalawi.com
DR MWALE