BOMA LISAMUTSA OGWIRA NTCHITO KU NYUMBA ZA CHIFUMU

Oweruza milandu ku bwalo lalikulu munzinda wa Blantyre a Chimbizgani Kacheche azapereka chigamulo pa 2 August chaka chino pa pempho la ogwira ntchito pafupifupi 100 omwe akutsutsana ndi chilinganizo cha boma chowatsamutsira ku makhonsolo ndi ku nthambi ya za mabwalo a milandu.

Posachedwapa boma linasamutsa anthu okwana 136 kuchokera ku nyumba zonse za mtsogoleri wa dziko lino koma ena mwa anthuwa okwana 99 omwe amagwira ntchito kunyumba ya Sanjika anakamang’ala ku bwalo la milandu potsutsana ndi ganizoli.

Mwazina anthuwa, omwe akuyimiliridwa pa mlanduwu ndi a Luciano Mickeus, akuti malingana ndi malamulo, iwo ndiwolembedwa ntchito yokhazikika ku nyumba za chifumuzi choncho nkosayenera kuwachotsako.

Iwo atinso anali odabwa ndi kalata yomwe analandira pa 23 May chaka chino yowadziwitsa zakusamutsidwa komanso osawuzidwa zifukwa zake. Izi zinakhudza state House ya Lilongwe, Blantyre, zomba ndi mzuzu

Pomwe bwalo limamva pempho la anthuwa lero, mlangizi wa boma pankhani za malamulo a Thabo Chakaka Nyirenda wapempha bwaloli kuti likane pempholi ponena kuti mwazina boma lili ndi ufulu kusamutsa ogwira ntchito ake ndikuwatumiza kumalo ena komanso anthuwa sanatsate malamulo ena pokamang’ala ku bwalo la milandu.

Ena mwa anthu okhudzidwawa ndi womwe amagwira ntchito zosamalira maluwa, aphunzitsi, osamalira mnyumba komanso achipatala.

Kusamutsa anthuwa kuwapititsa mu ma Khonsolo zikusonyeza kuti ma benefits onse omwe anthuwa anali nawo pa ntchito zawo ku Nyumba ya Chifumu athetsedwa (momveka bwino demotion)

“Vuto ndale zili paliponse, boma likangosintha ku nyumba ya chifumu kumasamutsidwa anthu ndipo kumayikidwanso ena. Koma ife chimene chatikhudza mchoti msamuko wake ndi odzidzimutsa ndiye ngati boma silingatibwenzere ku nyumba za chifumuzi kuli bwino tonse atipatse ndalama za chipepeso.” Mawu a mmodzi odandaula

Zambiri tsatani pa avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *