BOMA LIBWENZA NJINGA ZOMWE LAKHALA LIKULANDA AKABAZA

Kwanthawi yaitali boma lakhala likulanda njinga zamoto za kabaza mmaboma osiyanasiyana ka mba ka zifukwa zosakhomera,kupanda zipewa komanso kupanda laisensi.

Boma litamva kulira kwa anthu laganiza zobweza njingazi mwaulele. Malingana ndi nduna Yoona zachitetezo cha mdziko a Richard Chimwendo Banda ati tsopano aphunzitsa onse okwera njinga za kabaza ndikuwapatsa ziphaso zoyendetsera njinga za moto pa mtengo wa K 20,000 womwe kale unalipa K150,000 . Zomwe zikuthandauza kuti lachotsera ndalama yokwana 130,000.

Boma lati lipereka mwezi umodzi wa ulele kuti eni njingawa apange maphunzirowa ndipo kuchokera apo sazakhululukiranso munthu yemwe njinga yake ikhale yopanda zoyenereza komanso opanda chiphaso choyendetsera njingazi.

Poyamba boma linapereka miyezi itatu kwa akabazawa kuti akhomere njinga zawo koma analephera koma pano laperekanso mwayi wachiwiri kwa akabazawa ndipo lanenetsa kuti yemwe azengereze ndi zake.

Izi zikuthandauza kuti njinga zonse zomwe zili ku ma station apolisi zibwezedwa mwa ulele.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *