BASI YA TAM TAM IGWIDWA PA DEDZA

Kutsatira kanema yemwe wafala pa masamba a mchezo ku m’mawaku okhudza momwe basi ya TAM TAM imayendera, anthu akufuna kwabwino ananeneza dalaivala wa basiyi kupolisi.

Apolisi atamva za nkhaniyi anachita changu kulumikizana ndi anzawo pa dedza omwe anaimitsa galimotoyi. Iwo analankhulana ndi dalaivalayo za mayendedwe ake ndipo anaimbiranso mwini wake ma basiwa kumudziwitsa za mayendedwe a dalaivala wakeyu ndipo anamvana chimodzi.

Ma basi a TAM TAM akhala akuchita ngozi kawirikawiri mdziko muno kamba ka Kuyenda mosasamala. Apolisi ayamikira anthu omwe ajambula kanemayu ponena kuti apulumutsa miyoyo ya anthu ambiri ndipo akupempha amalawi onse kuti azineneza madalaivalawa kupolisi kuti tipewe ngozi za pansewu.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *