BAMBO WINA WAFA ATAGWERA MUCHIMBUDZI CHOKUMBA KU BLANTYRE

Apolisi mum’zinda wa Blantyre atsimikiza za imfa yabambo wina wazaka 46 yemwe wafa atagwera muchimbudzi chokumba.

M’neneri wa Polisi ya Limbe Patrick Mussa ndiye watsimikiza nkhani-yi ponena kuti ngozi-yi yachitikira kwa Kachere dzulo ndipo bamboyu dzina lake ndi Munana Mitambo.

A Mussa ati malemuwa adagwera muchimbudzi pomwe iwo amakoza denga la chimbudzi-chi kuti madzi amvula asamagwere mkati.

A Mussa apitiliza kunena kuti malemuwa anawatengera pachipatala cha Queen Elizatheth ndipo zotsatira zakuchipatala zaonetsa kuti malemuwa amwalira kaamba kovulala kwambiri m’mutu kutsatira ngozi yomwe inachitikayi.

Malinga ndi a Mussa a Mitambo anali ochokera m’mudzi mwa a Kachere mfumu yaikulu Machinjiri m’muzinda omwewu wa Blantyre.

AvantNewsFlash

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *