ANTHU OKWIYA NDI APOLICE APANGA ZIONETSERO KU MCHINJI

Ntchito zosiyanasiyana zinaima paboma ku Mchinji pomwe panali zionetsero zomwe anthu okhala paboma anachita chifukwa choti munthu yemwe anamangidwa ndi a police dzana anapezeka kuti wafa alimmanja mwa apolisi.

Apolisi anamanga munthu yemwe amamuganizira kuti ndi wakuba potsatira kuyendera malo apa boma usiku. Asanafufuze kweni kweni kunapezeka kuti woganiziridwayo wafa kucha kwa tsiku lachisanu.

Officer in charge wapa Mchinji police station, Charles James Mpezeni wati Innocent Konyo anali mchitokosi cha Apolisi kamba kakuba.

Malingana ndi apolisi, zotsatira zachipatala zasonyeza kuti Konyo yemwe ndiwadzaka 22 wamwalira kamba koti njira yomwe imadutsa mpweya simagwira bwino ntchito.

Konyo amachokera m’mudzi mwa chipezayani mfumu yayikulu Njolomole m’boma la Ntcheu.
Anthu ena okhala paboma amanena kuti apolisi anamanga munthu wolakwika komanso akuganiza kuti apolisi akukhudzidwa ndi imfa yamunthuyu.

Izi zinapangitsa anthu kupanga zionetsero zokwiya ndi apolisi. Apolisi nawo anakhwimitsa chitetezo paboma mpaka anathira utsi wokhetsa misozi.

Avant Publication yalandira mareport woti pomwe izi zimachitika, mzimayi wina wachitanso tsoka pomwe apolisi poponya utsiwu wakagwera panyumba yomwe ndi yofolera ndi udzu. Dzina la mayiyu ndi Eliza Tawuni. Nyumbayi yayaka ndikuononga katundu yense. Koma A Charles Mpezeni ati sanalandirebe dandaulo lililonse pangoziyi.

For details visit,

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *