Panali chisokonezo pa Mzuzu prison pomwe anamalira akufunsa ogwira ntchito pamalopa kuti afotokoze bwino chomwe chapha mbale wawo James Chimwaza amene amagwira ntchito pamalopa.
A Chimwaza amwalira dzulo madzulo akuti posatira kukangana chifukwa chanyumba zomwe zangomangidwa kumene pa Mzuzu prison.
Koma mmeneri wa ndende mchigawo chakumpoto watsutsa kuti a Chimwaza amwalira potsatira pokanganirana nyumba zaku ntchito. Iwo ati a Chimwaza anagwa nkukomoka nthawi imene anali kunyumba kwawo osati kuntchito.
AChimwaza omwe anali wochokera ku Kasungu anatsimikizika kuti amwalira atapita nawo kuchipatala potsatira kugwa ndi kukomoka.
Pakali pano anamalira ati Iwo satenga thupi lambale wawo kupita nalo kumudzi kwawo pokhapokha atauzidwa chimene chatenga moyo wambale wawo.
Avant Publications