PETER MPONDA WAYANKHURAPO ZA MASEWERO AWO APA UBALE KUMATHERO KWA SABATA INO

By: Innocent Mvundula

Wachiwiri kwa Mphunzitsi watimu ya Nyasa Big Bullets “Mapale” , Peter Mjojo Mponda walankhulapo pa zakufunikira kwa masewero awo opimana mphamvu amene ndi omaliza omwe aseweredwe kumathero a sabata ino. Mponda atafunsidwa ndi avant sports. Iye wati sanachite kusankha kuti asewere ndi matimu a chisirikari okha okha koma anangoganizira za kaseweredwe ka matimu wo ndi zimene iwo akufuna kupindulapo pa masewero amenewa.

Bullets isewera ndi timu ya Kamuzu Barracks loweruka pa CIVO stadium isanapite ku Dwangwa kukasewera ndi timu ya MAFCO pabwalo la Chitowe.

“Tasankha kusewera ndi Kamuzu Barracks podziwa kuti ndi timu yokhayo imene imamenya mpira wogunda ndi zimphamvu imenenso ithandizire kuwayesa anyamata athu dzitho ndi mthanana umene Alinawo pakali pano.
.
“Ndipo masewero a lamulungu ndi MAFCO atithandizire kuwona system yakaseweredwe yomwe matimu olowa kumene mu Super League akugwiritsa ntchito monga mukudziwa kuti ma team amene akumenya mu division amamenya mpira othamanga.” Anamaliza choncho Mjojo.

Zokonzekerazi zikubwera pamene mpira mdziko muno uyambe pa 21 November ndi masewero a mu chikho cha Ecobank Charity Shield. Bullets ikuyenera kudzakumana ndi timu ya Beforward Wanderers pa 21 November pomwe Silver Strikers idzasewera pa 22 November ndi Blue Eagles.Ndipo ma timu omwe adzapambane adzakumana mundime yotsiriza yamumpikisanowu.

Masewero onsewa adzamenyedwa opanda ochemelera ndi kuonera. Kodi FAM yakonza ndondomeko zotani kuti iike mpira pa kanema? Akungobwata koma palibe cha nzeru chikuoneka mpira ndi uwu ukuyambawu

*AVANT SPORTS ✍️🇲🇼

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *