Mphindi 90 zonse phuu, zadutsa ndipo Kamuzu Barracks yayimika manja m’mwamba kuvomereza kuti Chitipa United imadoda mpira.
Chigoli chimene chinabwera pa kudzera kwa osewera wa Chitipa United, Mabichi Msiska pa mphindi 18 chapangitsa Chitipa United FC kukhala ndi 20 points.
Izi zatengera timuyi kukhala pa nambala 3 mu TNM SuperLeague ndipo Mighty Mukuru Wanderers ili pa nambala 4 ndi 19 points. Ngati masewera otsatirawa Wanderers iluze, chitipa United itsogola ndi point imodzi
Kamuzu Barracks yabwerera ku Lilongwe opanda chigoli zimene zinapangitsa osewera a Kamuzu Barracks kukodzera pagolo pa Chitipa United mpira uli mkati.
Golo Boyi wa Chitipa United, George Chikooka ndi amene anali Man of the Match lero
Munali ndine
Vinjeru_Ngwira
AvantSportsDesk
Share this article