ophunzira a sukulu ya pulayimale kwa mtemwende ku dedza akunyanyala maphunziro kamba koti mnyamata wina yemwe anagwililira mwana wa sukulu mderali watulutsidwa pa belo.
Zomwe zinachitika ndi zoti mwanayo anakokeredwa mchimanga ndikumangidwa mpango kumaso kuti asamuzindikire munthuyo koma mmene amapanga izi nkuti atazindikirika kale.
Jaji yemwe amamva mlanduwu watumiza mlanduwu ku Bwalo la ana kamba koti mnyamatayo ali ndi zaka 17 ndipo mwanayo watulutsidwa pa belo.
Izi zakwiyitsa anawo kamba koti munthuyo amakhala pafupi ndi sukulu yomweyo.
Dera la mtemwende lili pakati pa chiluzi ndi mayani ku dedza komweko
www.avantmalawi.com
DR MWALE
Share this article