Malingana ndi mlili wa covid19 womwe wavuta kwambiri mmalawi Muno anthu ambiri akupanga njira zothandizira boma polimbana ndi mliliwu.
Apresident atalankhula kuti pakufunika chithandizo choti anthu athandize polimbana ndi mlili wa covid19 anthu ambiri achiona chanzeru potengapo gawo lomwe Iwo angakwanitse.
Tilowere ku Balaka komwe kwachitika chinthu chopatsa chidwi kwambiri pomwe anthu omwe ndi ochokera mu bomalo agwilizana zothandizira zosowa zapachipatala Cha boma lawo kuti athane ndi mlili wa covid19. Anthuwa anapanga group lawo matsiku atatu apitawa ndipo aliyense amasonkha malingana ndi nthumba mwake ,koma chotsangala ndichakuti mmatsiku atatuwa akwanitsa kusonkha ndalama pafupifupi 1.5 million komanso katundu wina othandizita ntchitoyo.
Mtolankhani wanthua Dr Mwale analankhula ndi oyankhulira gululi a Deus Sandram omwe atiuza kuti anthu aku balaka akhudzidwa kwambiri ndi mmene mlili wa covid19 ukufalikira ndipo anachiona chanzeru kuthandizapo kuti mavuto ena achepe. Iwo ati “atapanga gulu lawo, anakhala pansi ndikufufuza kuti pachipatala chanthuchi pakusowekera chani ndipo angapange bwanji kuti afikire?” ndipo atapeza anayamba kusokha limodzilimodzi.
Iwo ati mu gulu lawoli muli bwana mkubwa wa Balaka
komanso a DHO omwe akugwirira limodzi ntchitoyi.
Posachedwapa gululi likhala likupereka thandizo lawo kuchipatalachi.
Mr Sandram ati ndiokondwa komanso kuthokoza anthu akubalaka pamgwilizano wawo kamba koti nthawi zambiri WhatsApp imaoneka ngati chinthu chongochezera kapena chofalitsila mabodza koma Iwo achitenga chanzeru pogwilitsa ntchito whatsapp komanso Teregaram kulumikizitsa anthu omwe ndi akubalaka posonkhetsa thandizoli. a Sandram ati boma lililonse litha kupanga zomwe iwo apanga ndipo atha kuthandiza chipatala Cha kwawo ,osamadikira boma lokha pakuti nkhondoyi ndi yatonse.
www.avantmalawi.com
DR MWALE