TIKUMBUSANE ZA MBIRI YA EVISON MATAFALE.

Dzulo pomwe gulu loyimba la Black Missionaries linasangalatsa anthu ku Chileka mu Mzinda wa Blantyre, Ife pano pa avantmalawi tabwera ndi Mbiri ya Oyimbayu ngati Mbali imodzi yomukumbukira.

Evison Matafale anabadwa pa 24th November 1969, Iye anali Mtsogoleri wa Gulu loyimba la Black Missionaries lomwe linatchuka kwambiri ndi Nyimbo zawo mu Chimbale chotchedwa Kuyimba 1.

Evison Matafale anali Mtumiki ku Chipembedzo cha Marasta Ndipo anali ndi Dzingongo za Zitali zitali(Dread locks)

Mu Nyimbo zake, Iye ankakonda kuyika Uthenga omwe ankadzudzura Boma la Chipani cha United Democratic Front(UDF) pansi pa Utsogoleri wa Bambo Bakili Muluzi omwe pa Nthawiyo anali Mtsogoleri wa Dziko la Malawi.

Pa 24th November Mchaka cha 2001, Evison Matafale anamangidwa atalemba Makalata angapo odzudzura Boma. Koma pa Nthawiyo Iye anali akudwala Malungo.

Matafale ankadzudzura Boma la Bakili Muluzi kuti linkasamalira kwambiri Amwenye Achipembedzo cha Chisilamu pomwe eni nthaka anali pa Umphawi.

Matafale anatsekeledwa Mchitolokosi cha Apolisi mu Mzinda wa Blantyre, pomwe Iwo Apolisi anatsimikizira Mayi ake cholinga chawo kunali kungomufunsa Mafunso basi ndipo atulutsidwa Mchitolokosi.

Koma Usiku wa Tsikulo, Matafale anapita nawo ku Lilongwe komwe anakasungidwa Mchitolokosi cha Apolisi.

Pa 27th November 2001, Evison Matafale anamwalira ali M’manja mwa Apolisi, Zomwe Amalawi ambiri analoza Chala Apolisi kuti iwo ndiamene anapha Matafale.

Koma malinga ndi zomwe Dotolo Wamkulu pa Chipatala cha Kamuzu Central mu Mzinda wa Lilongwe anapeza, Atapima Thupi la Matafale, Iye anati Matafale anamwalira ndi Matenda a Chibayo.

Matafale anasiya Mkazi ndi Mwana M’modzi, Komanso Gulu lake loyimba la Black Missionaries.

Ndipo kumapeto a Mwezi wa November, Chaka chilichonse, Gulu lake la Black Missionaries Limayimba pa Bwalo mwaulere kwa Dadaga, Pafupi ndi Bwalo la Ndege la Chileka mu Mzinda wa Blantyre, Ngati Mbali imodzi yomukumbukira Evison Matafale.

Matafale anatchukanso ngati mneneri mmaimbidwe ake pomwe analotsera kuti nthawi ya kwana kuti mzinda wa New York uwonongedwe ,izi analankhula mu nyimbo yake yotchedwa time mark ndipo dziko linachitiraa umboni pomwe Osama binnladen anaonongadi mzindawu.

Atamwalira matafale black Missionaries imatsogoleledwa ndi Musamude fumulani yemwe naye anamwaliranso ndipo pano akutsogolera ndi anjiru fumulani.

Mtundu wa achina fumulani wapululuka kwambiri munthawi yochepa zomwe zadandaulitsa amalawi ambiri.tikukamba za Robert fumulani, Musamude fumulani, gift fumulani komanso band imeneyi yatayanso Rasta wina yemwe amaimba zida ku band Imeneyi nde gulu ili likamayima pa mwambowu limakumbukira anthu onsewa

Mizimu yawo onse iwuse mu Mtendere.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *