Mbava iwomberedwa ndi a Polisi

Apolisi awombera ndikupha chigandanga choopsa chitavulaza wapolisi wina pokana kumangidwa mdera la Makawa m’boma la Mangochi.

Mneneri wa Police ya Mangochi, Inspector Amina Tepani Daudi wati dzina lachigandangacho ndi Allen M’bwana yemwe m’mbuyomu anakhalapo mkaidi. M’bwana anali akusakidwa ndi apolisi ku Mangochi komanso ku Liwonde poganiziridwa kuti anathyola ndi kuba mnyumba zingapo mmaderawa.

A Tepani Daudi ati lero la Mulungu kumawaku apolisi aku Makokola anapita kunyumba Kwa a M’bwana anthu ena atawatsina khutu koma mbava yoopsayi inatenga nthawi isanatsegule chitseko.

A M’bwana atatuluka, asanayambe kuthawa anaponya mkondo wodzipangira wokha ndi kuvulaza wapolisi zomwe zinapangitsa apolisiwo kuombera mmwamba koma chipolopolo chinagwera aM’bwana omwe kamba kotaya magazi wochuluka amwalilira ku chipatala Cha Mangochi.

A Daudi ati wapolisi wobaidwayo akulandira thandizo kuchipatala.

(Dumisani Mwambazi-Mchinji)
17/03/24
avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *