WORLD HOPE CORPS MALAWI NDI MIRACLE FOUNDATION IPEREKA THANDIZO KU MAGANGA

Bungwe la world Hope  Corps Malawi (WHC) ndi limodzi mwa ma bungwe a ena omwe amagwira ntchito zachifundo pothandiza anthu osiyanasiyana mdziko la malawi kudzera mu ma pulojekiti osiyanasiyana.

Bungweli limathandiza anthu powapatasa madzi a ukhondo powakumbira mijigo yapamwamba kwambiri. Iwo amathandizanso anthu polimbana ndi matenda a HIV,  kulipira sukulu ana omwe ndi osowa komanso ndi zina zambiri.

Pofuna kuti ntchito za bungweli zifikire anthu ambiri bungweri lapanga ubale ndi Miracle foundation C.B.O ya ku Lilongwe kuti azigwirira ntchito limodzi. Ngati njira imodzi yofuna kutukulira ubalewu mabungwe awiriwa anapita ku Salima kudera la  Maganga mfumu yaikulu (T/A) Maganga komwe amakacheza ndi
anthu osiyanasiyana  makamaka kukamva ndikukaona zomwe anakumana nazo kamba ka ngozi ya madzi osefukira omwe anachitika kamba ka namondwe otchedwa Dumaku.

Wina mwa katundu yemwe wagawidwa kwa Maganga ku Salima

Pamwambowu mulendo olemekezeka anali Mr Dennis Singini m’kulu wa world hope Corps malawi amene anamvetsera mwachidwi za mavuto a anthuwa.

Mukulankhula kwa a khansala a derali  mayi Asiyàtu Chakwera anati   anthu awo anavutika kwambiri ndi madzi moti tikunena pano alibe chilichonse ndipo sakudziwa kuti adya chani kamba koti mbewu zawo zinakokoloka, ndipo ankhansalawa anati m’derali mulinso vuto lakusowa kwa madzi makamaka ku chipatala komwe amavutika kuti apeze madzi nthawi yofuna kuthandiza odwala monga amayi oyembekezera.

“Nalo denga lachipatalachi linasasuka ndipo mkati monse mumanyowa monga ino nthawiya mvura, zimbuzi zinagumuka ndipo anthuwa akusowa mtengo ogwira  ndipo ife tikupempha kuti mutithandize.” anatero mayi asiyatu chakwera

Amfumu a maganga nawo anagwirizana ndi  zomwe akhansala wa komanso anthu a m’mudziwo analankhula ponena kuti chisefukureni madzi muderali mwabuka matenda osiyanasiyana kamba koti akumwa madzi osayenera zomwe zikuikanso moyo wawo pa chiopsyezo.

Mkulu wa miracle foundation a Steven Chinsendenji nawo analimbikitsa anthu aku maganga kuti asadere nkhansa chifukwa mavutowa sikutha kwa moyo koma chiyambi cha moyo wina ponena kuti iwo ndi Miracle  foundation agwira ntchito yothandiza kutulula Deralo ndipo apempha achinyamata a deralo kuti agwirire ntchito limodzi.

Mr Deniss Singini anakhudzika kwambiri ndi mavuto a anthuwa ndipo anachita chotheka kupita kukaona chipatala chawo chomwe akuti chinamangidwa 1986 koma mpaka pano sichinakonzedwepo momwe munaonongeka, Mr singini  analowa muzipinda zonse za chipatalachi mpaka komwe akuchirira azimayi (komwe kunalibe odwala panthawiyi) kuti akaone mmene kulili zomwe  zaonetsa kuti anthuwa alidi pa mavuto.  Avant publications ndi mtolo nkhani wanthu ekari anali nawo pa ulendowu ndipo ajambula zonse, Mr Singini ati a sakufuna kulonjeza koma amva ndipo bungwe lawo ndi Miracle foundation awona kuti angatani kuti abale anthu apeze madzi pachipatalapa ndikukonza denga  komanso zimbudzi zoonongeka

www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *