Olemba Dr Mwale
_KULI ZII🤔_
Avantmalawi yakhala ikutsatira bwino, komanso kudikira tsiku la chigamulo la Mulandu umene a Enock Chizuzu, Kafandikhale Mandevana komanso a Foster Thipiwa anasumila Bungwe la MEC. Kutsutsana ndi kupambana kwa a Francis kansaira komanso a Esther Mcheka Chilenje kungotchulapo ochepa.
Pamene miyezi yadutsa, opanda Chilungamo kutsatidwa bwino. Boma latsopano la Tonse lidakali munjira kupita Ku Canaan.
Avant inakwanitsa kulankhula ndi Lawyer oyimira odandaula (A Kosaam) yemwe nayenso sakudziwa tsiku la chigamulo.
Izi ndi zinthu zoseketsa komanso zopatsa chidwi. Kapena tiziti a Judge oweruza analandira ziphuphu kuchokera kwa a Esther Chilenje komanso a Francis Kansaira?
Ife ngati nyumba yofalitsa tili ndi chidwi pankhaniyi. tiziti ku Nsanje zitukuko zikupitilira kapena zangoyima malinga ndi milandu komanso mpungwe mpungwe ulipo?
Chomwe chinachitika ndi chakuti bwalo la milandu linamaliza kumva mlandu ndipo linapereka matsiku 50 kwa ma maloya onse kuti apereka zikalata zawo zomwe akuzitchula kuti submission koma izi zidachitika kale kale ndipo odandaula akudabwa kuti Kodi ma Judge omwe akumva mulanduwu akudikira chani poti sanapereke tsiku lomwe azapereke chigamulo. Nkhaniyitu yadabwitsa odandaula ndipo zapereka chikaiko ndimaganizo oti mwina nkutheka odandaulidwa anapereka ziphuphu kwa oweruzawa, nanga ndichifukwa chani sakupereka tsiku lachigamulo pomwe zonse zinatha kale? Apa odandaula akuti izi zikuonetsa poyera kuti odandaulidwa anagula nthawi ndicholinga choti a mcheka chilenje ndi anzawo azikhalabe pa mpando.
Chodabwitsa ndi chakuti ma loya oyimira odandaula nawo sakupita ndikufunsa ma jaji za nkhaniyi. Kodi akuopa chani? Kapena ndi malamulo kuti sakuyenera kufunsa?
Mlanduwu watenga nthawi ndipo unachitikira limodzi ndi wa apresident koma mpaka pano kuli zii! Kuchedwetsa kupereka chigamulo kukhudza kwambiri Dera la aphunguwa pa nkhani ya chitukuko chifukwa pazikhala kulimbana komasno kusasangalatsidwa ndi chitukuko Cha munthu yemwe sakumfuna.
Avant publications ikupempha mkulu wa ma bwalo a milandu a chief justice a Andrew Nyirenda kuti athamangitse milandu yonse ya chisankho kuti chisankho chachibwereza chizachitikire limodzi.
Malawi waziwika dziko lonse ndi kuweruza nkhani zachisankho mwachilungamo nde iyi isayipitse mbiri ya ma jaji athu abwinowa.
A president komanso akulu akulu mgwilizano wa Tonse pangani machawi kuti muthandizire odandaula pa mlanduwu kuti chilungamo chioneke ndipo Tonse tikhale mu kenani
www.avantmalawi.com
Chinyengo sichingathe pa malawi,owina ndiyemwe wadandaulayo.