Kudali mpungwe pungwe ku Dedza pomwe ophunzira okwana 22 omwe sakulemba nawo mayeso anayamba kuchita ziwawa pa centre ya Malemba.
Ophunzirawa sakulemba nawo mayeso chifukwa choti mphunzitsi wawo wa mkulu sadakapereke ndalama yolipilira mayeso ku Maneb yomwe anawa anapereka.
Ndipo iwo atafika ku malowa kuti akatenge ndalama zawo kwa mphunzitsi wamkulu koma atalephera kubwezeredwa ndalamazi, anawa anayamba kugenda pa malowa.
Izitu zinapangitsa anthu enaso a m’mudzi kuyamba kuchita nawo zomwe anawa amachitazi.
Pakadali pano akulu akulu oyendetsa mayeso pa malowa asintha malo olembera mayesowa nkupita ndi olemba mayesowa ku Phokera komwe akulemberako mayesowa.
Anawa anenetsa kuti sachoka pa malopa kufikira atabwezeredwa ndalama zawo.
Share this article