MVULA YAVUTA KU TUKOMBO

Chaka chino Madera ambiri akulandila mvula yamphamvu kamba ka kusintha kwa nyengo. Posachedwapa taona chigawo cha kumwera kukugwa mvula yomwe yaononga zinthu ndi miyoyo ya anthu oposera 1000. Kamba ka namondwe wa Freddy.

A nthambi yoona za nyengo analengeza kuti mvula ya mphamvu izigwa mmadera a mmbali mwa nyanja.
Pakadali pano ma report omwe Avant publications ikulandila ndi oti mvula yomwe ikugwa ku Tukombo mu boma la nkhatabay ikudetsa nkhawa kamba koti ikungogwa mosalekeza. Mmodzi mwa anthu onwe talankhukana nawo ku Tukombo ati manyumba ena ku camp ya tukombo agwa komanso zimbuzi zochuluka zagwa komanso zadzadza madzi. Tikunena pano derali lakhala kopanda magetsi kwa matsiku oposera anayi.

Bola likupempha anthu a muderali kuti akhale Osamala kamba koti madzi alowa kwambiri pansi zomwe zingapangitse kuti manyumba ambiri agwe.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *