Miyezi yapitayo boma linachotsa Ntchito anthu ena ogwira ku nyumba ya Chifumu mu nzinda wa Zomba, Blantyre (Sanjika) komanso Lilongwe (State House.) Lero ku nyumba la chifumu ku Zomba kunabwera galimoto limene limayembekezera kusamutsa anthuwa kukagwira ntchito kwina kuchoka ku Nyumba ya chifumuyi.
Izi sizinakondweretse wena mwa anthu amene akusamutsidwawa amene akufotokoza kuti Nkhani yakusamutsidwa kwawo ili ku bwalo la Milandu kumene iwo akudikira chigamulo.
Ena mwa anthuwa anathamangira ku Police kumene amakadandaula kuti athandizidwe chifukwa akusamutsidwa mopanda dongosolo.
“Tangowona lorry imene yabwera kuti tikusamutsidwa, koma amene abwera sanafike mwa ulemu, akutimenya komanso akumalowa mmanyumba mwathu mwa mphamvu. Izi zatipangitsa kuti tipite ku Police tikadandaule. Kusamukako sitikukana koma sitinalandire makalata akuti tinapatsidwa ntchito kwina ndiye tisamukira kuti?” Kulankhula kwa Mmodzi mwa ogwira ntchito kunyumba ya boma ku Zomba
Anthu oposera 150 ndi amene anakhudzidwa ndikusithidwa ntchitoku miyezi ingapo yapitayi, ndipo anthu onsewa anamang’ala kubwalo la milandu. Anthuwa padakali pano sakugwira ntchito komanso sakulandira malipiro ndipo Boma silinalankhulepo za Nkhaniyi.
Tsatani AvantNewsFlash