Bwalo lamilandu ku Mzuzu lagamula mnyamata wazaka 19 kukakhala kundende kwa zaka 19 atampeza wolakwa pamlandu wogwirira msungwana wa zaka khumi ndi zitatu.
Mnyamatayu ndi Griffin Mbewe, ndipo powuza bwalo lamilandu mboni ya boma, Sergeant Christina Shadreck anati awiriwa anali pa ubwezi ndipo izi zinachitika msungwanayu atagona kunyumba ya wolakwayu.
Malingana ndi mboni yabomayi makolo awiriwa akhala akuwachenjeza koma iwo adasankha kusatsatira.
Iye anapitiliza kuuza bwalo lamilandu kuti msungwanayu pano ndiwoyembekezera choncho mnyamatayu apatsidwe chilango chokhwima.
First Grade Magistrate Makayika anagwirizana ndi mbali yaboma choncho analamula mnyamatayu kukakhala kundende kwazaka 14 ndikukagwira ntchito yakalavula gaga.
Iye amachokera mmudzi wa Manja kwamfumu yaikulu Chikwewu m boma la Machinga.