MBIRI YA KATSWIRI WA ZISUDZO OTCHEDWA MULELEMBA

Ambiri timakudziwa kuti Mulelemba koma dzina lake lenileni ndi Aubrey Isaac Mafumu Matiki.Iyeyu ndi katswiri wa zisudzo ndi nthabwala,oimba komanso mphunzitsi wa ku University.

Mulelemba amachokera mu boma la Chiradzulu.Adaphunzira m’sukulu zambiri monga Biwi,St Pius,Nsodi.Kenako anapita ku Tsabango CDSS.Atamaliza secondary anapanga za Public Relations,Chartered Marketing and Strategic Management.Kenako Mulelemba anabwelera kusukulu kawiri kumene anapitiriza mpaka kukatenga degree (Bachelor Of Arts In Business )ku University ya Malawi.Panopa akupanga Masters Degree in Development Communication ndipo iyeyu tikunena pano ndi mphunzitsi wa ku University ku Polytechnic komanso ku College Of Medicine (Now Kamuzu College Of Health Sciences).

Mulelemba anayamba zisudzo Ali mwana ku primary ndipo wapanga mu magulu azisudzo ambiri m’Malawi muno.Mkuluyu ngokwatira ndipo alinso ndi mwana amene ndi rapper dzina lake Princess amene panopa Ali ku University Of Malawi(Chanco) mu chaka chotsiriza ndipo akupanga Bachelor Of Arts In Communication Cultural Studies.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *