Nkhani ya mneneri wotchuka a Bushiri yakhala ili mkamwa mwa anthu dziko lonse lapansi kamba ka milandu yake ku dziko la South Africa komanso kamba ka mayendedwe ake kuchoka ku South Africa kubwera ku Malawi.
Wonder msiska mtolankhani wa times anacheza ndi Bushiri kwa pafupifupi mphindi makumi atatu ndipo Avant publications yatengamo mfundo zofunikira pa mchezowu.
Poyamba Wonder anafunsa kuti zidakhala bwanji mdziko la South Africa?
apa mneneri Bushiri anafotokoza kuyambira pachiyambi za mlandu wake kuti dzikolo lili ndi apolice ena achinyengo omwe amafuna kuti Bushiri awapatse ndalama zokwana 10, million rands zomwe kwanthu kuno ndi pafupifupi K500 million. Iye wati apolisiwa amabwera tsiku lililonse kunyumba kwakwe kumafunsa za ndalamazi ndipo amati ngati sawapatsa iwo amutsegulira mlandu.
Nkhaniyi inayamba mchaka Cha 2018 ndipo amamuopsyeza kuti iye ali ndi mlandu mdzikolo. Bushiri atamva zoti ali ndi mlandu anapita yekha ku police ya dzikolo kukafunsa ngati alindi mlandu koma wankulu wa police mdzikolo anakana kuti sakudziwapo chilichonse komanso kupolisi kulibe failo ya mlandu wake (Bushiri Andi ndi makalata omwe anamulembera wankulu wa polisi) Izi zinadabwitsa mneneriyu mpaka kukasuma ku bwalo la milandu kuwasumira apolisi achachinyengowo koma palibe chimachitika.
Wonder anafunsa kuti ndichifukwa chani munamangidwa? Bushiri anayankha kuti nkhani yaikulu ndi momwe anagulira ndege yake poti anapereka ndalama cash komanso Zina anatumiza kudzera ku bank. Koma atafunsidwa kuti ndichifukwa chani anamanganso nkazi wake, iye anayankha kuti naye ndi odabwa kuti za ndege zikukhuza ine ndamene ndinagula nde mkazi wanga chikumukhuza ndi chani? Dziko lonse lapansi limadziwa mlandu opalamula mwamuna nkazi sangamangidwe nde south Africa imaonetseratu kuti inali ndi mangawa ndi ine.avant publications
Bushiri anapitiliza kunena kuti ali ndi umboni wa ziwembu zonse zomwe apolisi aku south Africa amamuchitira, pofuna kumuombera mu Church, pa filling station (times imaonetsa ma vedeo) komanso kumuikira poison kuchakudya chake komanso mkazi wake.
kodi mneneri munayenda bwanji pobwera kunoko?
poyamba ndipepese kwa apresident adziko lino kamba ka zomwe zinachitika chifukwa tinanyazitsa mbiri yawo komanso dziko lino, a president ndimawalemekeza kwambiri, koma ine sindinabwere ndi a chakwera, mmene ndimalengeza kuti ndili kuno achakwera anali ku South Africa zomwe anawapanga apresident ku South Africa zikukuonetsani amalawi kuti anthu aja ndi ankhanza.
Koma chabwino anthu akufuna kudziwa kuti munabwera bwanji kuno?
Mneneriyu anayankha funsoli mokuluwika pogwilitsa ntchito mkuluwiko ndipo anati ” ngati nyumba ikupsya ndipo anthu ali Momo ndipo mwamwayi ena apulumuka kuwafunsa kuti munatuluka bwanji akuuzani kuti sindikudziwa ,mwina ndichisomo Cha mulungu ndipo nane mmene ndinatulukira sindikudziwa ndipo ndichisomo ,Kaya ikhala miracle koma inenso sindikudziwa”
Bushiri anakana mpheketsera yoti iye anabwera ndi anthu omwe amabwera ku maliro a Ginimbi ku Zimbabwe ndipo chenicheni pa zamayendedwe ake sichikudziwika.
Bushiri wakana kuti iye sapitanso ku South Africa kamba koti anthuwo sakamuweruza mwachilungamo Kaya atenga katundu wake alibe nazo ntchito.
Pankhani yoti mwana wake akudwala ndipo akufuna kumutumiza kunja koma iye ndi mneneri yemwe amapempherera anthu kuti achire pa mwana wake zikulephereka bwanji? Mneneriyu anayankha mogwilitsa ntchito Baibulo ndipo anati aliyense amadwala ndipo azafa,kukhala mneneri sikuthandauza kuti iye kapena wakubanja kwake sangadwale ndipo sazamwalira, mwana wake anabadwira kuchipatala ndipo athakupitanso kuchipatala kukalandira thandizo kamba koti mpingo wake suletsa munthu kupita kuchipatala, koma choti mudziwe avant ndichakuti mwana wake kuti afike pamenepa ndi chisomo chifukwa vuto lake linayamba kale kale ndipo akhala akumupempherera.
Pomaliza bushiri wauza anthu onse kuti iye sanathawe mlandu koma amapulumutsa moyo wake ndipo akuyembekezera kuti kuno kumalawi mulandu wake uyenda bwino komanso mwachilungamo ndipo iye ali okonzeka kukaima pa maso pa bwalo ndi maumboni ake onse omwe ali nawo ndipo zitengera bwalo la Malawi kuona kuti iye ndiolakwa kapena ayi.avant publications
Mmene pologalamuyi imaulusidwa nkuti anthu aku south Africa akutsatira mwachidwi ndipo ngakhale samamva Zina mu chichewa koma Iwo akuti ali pambuyo pa bushiri ndipo mulungu akanthe anthu onse omwe akuzunza bushiri.
www.avantmalawi.com
DR MWALE