Bwalo la milandu mdziko la Nigeria lalamula kuti Mustapha Idris wa zaka 29 aphedwe ponyongedwa ndi Chingwe Kamba koti iyeyo anapha bwezi lake yemwe dzina lake ndi Nafisa Hashimu.
Bamboyo anafotokoza kuti anapha bwezi lakelo Kamba koti bwezi lakelo linali ndi mimba (pa nthupi) ya miyezi iwiri, iyeyo amkachita manyazi kuti anthu adzamuseka akazazindikira kuti ali ndi mwana yemwe anabadwa kunja kwa banja asanakwatilane choncho iyeyo anaganiza zokupha bwezi lakelo Pofuna kubisa mimbayo.
Share this article