BWATO SATSITSILANA PAKATI PA NYANJA

Pomwe wachiwiri kwa president wa dziko lino ali ku South Africa kugwira ntchito za boma, Nduna yowona zokopa alendo yomwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM, Michael Usi anaimira president wachipanichi a DR Chilima pa mwambo okumbukira president oyamba wa dziko lino Ngwazi Hasting kamuzu Banda omwe unachitikira ku Lilongwe.

A Michael Usi omwe nawo atengera miyambi ya Chilima anauza anthu otsatira chipani cha MCP komanso President Lazarus chakwera kuti chipani cha UTM chilibe lingaliro lotuluka mu mgwilizano wa Tonse alliance ngakhale pali kagulu kena komwe kakufuna zinthu zitero. Iwo anati bwato satsitsirana pakati pa nyanja kuthandauza kuti mgwilizano sukufunika kuthera panjira, koma kuti tonse tikafike.

A Usi ati kukakamiza chipani cha UTM kutuluka mu mgwilizano wa Tonse mchimodzimodzi kukakamiza munthu kuti atsike mu bwato lili pakati pa nyanja. Iwo anenetsa ponena kuti UTM ipitiliza kulemekeza mgwilizano wa Tonse ndi mfundo zake zonse mpaka nthawi yoikika.

Ndunayi sinasiyire pompa koma inauzanso mtsogoleri wa dziko lino a Dr Chakwera kuti achotse ntchito kagulu kena ka anthu komwe kakufuna kusokoneza boma lake. mmawu ake a Usi ati “kalipo kagulu ka anthu ena komwe ntchito yake ndikufuna kukusocheretsani, musazionerere izi, anthu amenewa achotseni chifukwa akulepheretsa mwa dala zitukukuko zomwe boma la tonse linakonza kuti lichite.” Anatero a Michael Usi

Mawu awa akubwera kamba koti akulu akulu ena a MCP ayamba kale kukamba za yemwe azaimire chipani cha MCP muchisankho cha 2025 mmalo molimbana ndikukonza zomwe zikulakwika.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *