Potsatira kuphedwa kwa a Sebastian Nkhata zipolowe zinabuka pa Mzambazi trading centre ku Mzimba dzulo zomwe zaonongetsa katundu wochuluka komanso kupangitsa anthu ambiri kuthawa pamalopo.
Monga mwa nkhani zathu za dzulo zomwe Avant Publication inakupatsirani a Sebastian Nkhata a zaka 35 anaphedwa potsatira ndeu imene anaiputa dzulo.
Apolisi ati a Nkhata anabaya a Masamba omwe amasoka pa msika wa Mzambazi kamba koti anali pa ubwenzi ndi chibwenzi chawo cha kale chomwe iwo(aNkhata) anachipatsa mwana zaka zitatu zapitazo koma sanakwatirane. Mkaziyo anapeza a Masamba pofuna kumanga nawo banja.
ANkhata pomva izi anabwera ndi mipeni kudzathana ndi a Masamba. Amayi ena podzudzula izi, a Nkhata anayamba kumenyenso a mayiwo zomwe zinakwiyitsa anthu ochita malonda pamalopo omwe analowerera ndikumenya aNkhata. Ankhata anafera pompo.
Anthu a mmudzi mwa Nkhweta komwe ndi kwawo kwa aNkhata atamva zankhaniyi anabwera pa msikapo ndikuyamba kubaya komanso kumenya anthu apamalopo ati pokwiya ndi imfa yam’bale wawoyo.
Malipoti akuti apolisi aku Euthini atafika pamalopo analephera kukhazikitsa bata pamalopo ndipo anathawanso zimene zinapangitsa kuti apolisi a paboma pa Mzimba afike kumaloko.
Mmene Avant Publication imalandira nkhaniyi nkuti anthu ammudzi mwa Nkhweta atathawa pamalopo komanso mmudzi mwawo kukabisala kutchire.
(Ma audio akufotokoza zomwe zinachitika mChitumbuka)
(Reported by Dumisani)
For details follow
www.avantmalawi.com
Shared on avantmalawi.com