ACB yavuta ku immigration Department ya Lilongwe

Mmawa wa pa 11 July 2024 kunavuta ku immigration Department pamene bungwe la Anti-Corruption Bureau lanenetsa kuti salora chinyengo chilichonse ku Bungwe lopanga ma passport ku Lilongwe.

Bungwe lothana ndi ziphuphu lati lamanga anthu amene akukayikilidwa kuti amabera anthu powalipilisa ndalama mwachinyengo zowonjezera kuti athandizidwe.

Bungweli lati passport ya ordinary ndi K50,000 ndipo passport ya express (pompo pompo) ndi k120,000 ndipo pasapezeke wina wotenga ndalama zowonjezera pamenepo.

Polankhula oyimira Immigration Department (omwe amasindikiza ma passport) ati ma boma onse mu dziko la Malawi akupanga ma passport ndipo anthu asakhamukire ku Lilongwe. Iwo amema anthu kubwerera mma boma awo monga Blantyre, Mzuzu, Mangochi ndi ena kukatenga kapena kukapangitsa ma passport awo.

Hilary Chilomba amene akugwirizira mpando wa ACB watsimikiza kuti anthu 8 amangidwa kutsatira ziphuphu ku Lilongwe. Pa anthuwa asanu ndi ogwira ntchito ku Immigration ndipo atatu ndi ma dobadoba.

Bwana wa ACB wati mmodzi mwa anthuwa anapezeka ndi ndalama zochuluka komanso ku akaunti kwake kunali 2.5million. ACB sinapereke mayina a anthu amene amangidwawo

Bungweli lati ligwira ntchito limodzi ndi ACB kuyambila lero pofuna kuthana ndi ziphuphu.

Zambiri tsatani Avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *