Mmodzi mwa akulu akulu a chipani cha DPP a chimwemwe chipungu ati kuchoka kwa mkhala kale pa ndali a Brown mpinganjira mu chipani cha DPP sikusintha kalikonse ndipo iwo ati chipani cha DPP sichiwasowa mpinganjira.
Iwo ati kubwera kwawo mu chipanichi sikunasinthe kalikonse ndipo kuchoka kwawo sikunasinthenso kalikonse. Ampinganjira amadziwika bwino ndi kusinthasintha zipani ndipo iwo amakha mbali yolamula nthawi zonse. Poyamba mkuluyi anali wa MCP kenako anasintha kulowa UDF komwe anakhalako zaka zochuluka, Bingu atalowa muboma iwo anachoka mu UDF kukalowa DPP , mkuluyi anayambitsa chipani chake chotchedwa NDA chomwe sichinaphule kanthu angakhale iwo anaimirapo ngani president. Chipanichi sichikudziwika kuti chinatha bwanji pomwe ochisogolera wake akungosintha zipani.
A mpinganjira abwerera ku MCP ndipo sitikudziwa kuti boma likasintha. Ampinganjira azalowera kuti?
www.avantmalawi.com
DR MWALE