Sitima ya titanic inapangidwa kwa zaka ziwili kale kale. Sitimayi inayamba kupangidwa mu 1909 ndipo inatha mu 1911. Inayetsedwa ndipo zonse zinali mu chimake. Mu chaka cha 1912 pa 10 April sitimayi inayamba ulendo wake wa pamadzi ndipo inanyamula katundu wambiri komanso anthu okwana 2100 kuphatikizapo mwini wake yemwe anapanga sitimayo. Ali pa ulendo wawo. Pakati pamadzi oyendetsa sitima analandila uthenga kuti kutsogolo kwake kuli madzi omwe anali owuma ndipo akuoneka ngati chimwala. (Ice block) Choncho mukuyenera muwalewe. Koma mmene uthengawu umafika nkuti sitimayi itayandikira kale malowo ndipo zinali zovuta kuti chinthu chachikulu ngati ichi chomwe chimathamanga kwambiri chiyime kapena kukhota mwadzidzidzi. Panalibe kuchitira mwina koma sitimayo inawomba madziwo ndipo inabooka.
Sitimayi itaomba madziwo sikuti inaima pompo ayi, inayendabe mtunda wautali koma inali itabooka kupansi kwake ndipo pang’ono pang’ono madzi anayamba kulowa. Uthenga unatumizidwa ndipo anthu opulumutsa anabwera. Sitimayi inatenga pafupifupi maola awiri kuti imire, panthawiyi nkuti anthu ena atayamba kupulumutsudwa koma ena samadziwa kuti kukuchitika chani. Anthu okwana 700 ndamene anapulumutsidwa ndipo anthu okwana 1400 anamwalirira momwemo.

KUKAIONA KOYAMBA TITANI
Itamila mu chaka cha 1912 panalibenso munthu aliyense yemwe anakaiona sitimayi. Mpaka mu chaka cha 1985 pomwe Robert Ballard anapita koyamba kukaiona patadutsa zaka 70 ili pansi pompo. Iye anakaiona ndikujambula zinthuzi ndipo anabwerelapo wamoyo.
kuchokera pompo anthu ambiri akhala akupitapo pamalopo ndikumabwera a moyo. Monga james Cameron anapitapo maulendo okwana 33 mu chaka cha 1995. Iye amakatenga zithunzi zomwe anagwilitsa ntchito mu filimu yake yotchedwa titanic. Ndipo mpaka pano James Cameron ali moyo.
CHIDACHITIKA NDI CHANI KWA ANTHU ASANUWA?

Azungu amakonda kumakaona Malo osiyanasiyana, monga timadziwira, ku ulayako kuli kampani Ina yomwe imakonza mayendwe okaona zinthu pansi pa nyanja, anthu ena olemera anabuka kampaniyi kuti iwo akufuna kukaona sitimayi ndipo awakonzere mayendedwe. Kampani yotchedwa ocean gate inapanga chombo chawo ndipo atachiyesa zonse zinali bwino. Anthuwa analipira $250,000 pafupifupi K250, billion zakwathu kuno. Ulendo unayambika ndipo iwo amayembekezeka kukakhala pansipo kwa matsiku osapitilira anayi. Koma atafika pamalopo madzi amayenda mwa mphamvu kwambiri ndipo chomboyo chinalephera kupirira, network inasokonekera. Sitimayo ili pa mtunda wa ma kilomita okwa 3.81 kuchokera pa mwamba pa madzi. (Tangoganizani mtunda wa makilomita atatu mdera la kwanulo). Kachomboka kanasweka kamba ka mphavu ya madzi pansipo ndipo ndizachidziwikire kuti katasweka madzi analowa ndipo anthu onsewo anamwalira. Timagalimoto toyendera limoti titapita pansipo kukapulumutsa anthuwo tinajambula tiziduswa ta ka chombo komwe anakwera anthu tili patali ndi pomwe pali sitimayi izi zikusonyeza kuti anthu anakokoloka ndi madzi amphamvuwo basi anapita.avant publications ikutero.

KODI SITIMAYO ILI BWANJI?
Pano ndi pafupifupi zaka 111, chimilireni ndipo sitimayo ili chiyimire pamalopo koma zitsulo Zina zinaphwasuka komanso zinapanga dzimbiri kwambiri kamba ka madzi a mchere. Izi zinapangitsa kutu sitimayi iduke pakati, ndipo izi ndi zomwe zikulepheretsa anthu kuti ayikoke chifukwa kungotero yonse iphwasuka. Koma maganizo okokawo alipo ndithu.
KODI ANTHU AFAWO ANATUMIDWA?
Anthuwa sanatumidwe koma anapita mwakufuna kwawo, ndipo kampani ya Ocean gate ilibe mulandu. Pankhaniyi. Mmodzi mwa mkazi wa anthu omwe amwalirawo ndi chidzukuku cha zidzulu za omwe anamwarira mu sitima ya titanic ndipo lero mwamuna wake wamwalira pofuna kukaona sitima yomweyo. Munthu yemwe anapanga titani anamwalira ndi sitimayi ndipo lero yemwe anapanga chombo cha ocean gate naye wamwalira mu chombochi pofuna kukaona sitimayi ndichifukwa Avant publications ikunena kuti Sitima ya titanic ikupilira kupha anthu

www.avantmalawi.com
DR MWALE