OGWILA NTCHITO KU TIGER FLOUR COMPANY AKUZUNZIKA

Olemba Dr Mwale

Ogwira ntchito ku kampani ina yopanga ufa ku Brantyre yomwe imaziwika bwino kuti TIGER FLOUR COMPANY yomwe ili pafupi ndi kampani ya bakhresa moyang’anizana ndi Right price whole sale adandaula ndi mchitidwe wa ma bwana awo omwe akuti akuwazunza mukagwiridwe ka ntchito yawo.

Kampaniyi ikupanga ufa ndipo eni akendi amwenye. Mwini kampane imeneyi dzina lake ndi MR MALIDA ndipo bwana wankulu ndi MR LIMBADA www.avantmalawi.cogwira ntchitowa adandaula kuti akangolakwitsa pang’ono mabwana achimwenyewa akumawamenya zomwe sizikuwatsangalatsa chifukwa akangobwezera atha kuzaimbidwa mlandu chifukwa anthuwa ndi andalama koma pa malamulo a boma lathu sakulora kuti ogwira ntchito azimenyedwa ndi mabwana chonsecho ndi obweranso.www.avantmalawi.com

Anthu ena atha zaka zinayi akugwira ntchito mwa ganyu koma osalembedwa mwa tikiti, pamene ena akungofikira pa tikiti.
anthu ambiri pa kampani imeneyi amagwira ntchito mwa ganyu ndipo amalembedwa ntchito madzulo amatuluka mmawa ndikupatsidwa ndalama zawo koma zachisoni munthu amayendera K100 pa ola limodzi koma anthu akuwalemba ganyu amakhala omwewo Kodi zimavuta pati kutilemba ntchito ndikumatipatsa ndalama ngati enawo?anadandaula chotero mmodzi mwa anthu omwe analankhulana ndi Avant publications.
Ku Tiger kampane munthu olembedwa mmawa ganyu kutuluka madzulo amalandila K1300 ndipo usiku amalandira K1500

Chonyasa kwambiri ndi chakuti ikakwana nthawi ya chakudya Cha masana anthuwa amatipatsa ma buscuit omwe amakhala oti anapanga kale expire.komanso anthu ogwira ntchito tsiku lonse sangakhute buscuit ndikumagwiranso ntchito ,izi ndi nkhaza zazikulu zomwe kampaniyi ikuchita ndipo tikupempha boma kudzera mu unduna owona za mdziko komanso unduna owona za ufulu wa anthu ogwira ntchito kuti alowererepo chifukwa tsiku Lina ogwira ntchitofe tizatopa ndipo tizapanga chinthu chomwe mabwanawa sazachikonda, boma lizatiyesa ife olakwa koma apapa tikufuna zithu zisanafike poyipa mutithandize. Watero ogwira ntchito wina yemwe wakana kuti tisamutchule dzina.

Inafika nthawi ina tikalowa mabwanawa amatikhomera pakhomo iwo ndikumapita nkuzatitsekulira akabwera.chonsecho momwe tigugwira ntchitomo mulibe ma window. Kodi Moto utayaka ife tili Momo zingakhale bwanji? Tiyamike mulungu kuti patatha matsiku anayi anyamata anatsowetsa loko moti pano sakukhoma.

Munthawi ya DPP kunabwera anthu oyezayendera koma asanabwere amawadziwitsa kaye eni kampani kuti tikubwera zomwezimapangitsa kuti asanabwere onse ogwira ntchito mwa ganyu aziwabitsa kuti asaoneke. ndipo oyenderawo potuluka anawapatsa matumba a ufa angapo aliyense ndipo sanabwerekonso mpaka lero.

Mmene boma lasinthamu www.avantmalawi.c ndi chiyembekezo chathu kuti abweretsa azayendere kuno modzidzimutsa kuti azaone mmene zinthu zilili kuno.
www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *