NKHANI ZA MPIRA

Mavuto osasimbika atha kubuka ku team ya silver strikers ngati ingayelekeze kugonja ndi team ya be forward wanderers loweluka lino pamasewelo omwe atachitike ku kamuzu stadium ku Blantyre

Kusatila ndi kugonja mmanja mwa team ya civo lamulungu lapitali 2-1;mu Lilongwe derby ena mwa akuluakulu amasapota a team ya silver Ali okwiya ndi zosatila idzi.

Anthuwa ati zinthu zina ku silver sizikuyendako bwino ayi anthuwa awonjezela kuti ziganizo zambili ku silver zikuchitika mosatsata ndondomeko ayi iwo ati monga kuchosedwa kwa osewela ena komwe kwachitika chibweleleni phunzitsi wasopano waku zambia bambo kabwe

Ndipo zinthu zitha kuvuta ku silver ngati ingayelekeze kugonja ndi wanderers loweluka likubwelali pa kamuzu stadium.

Kwa onse omwe anali ndimalingalilo oti atenge mphavu yolamulila masapota a team ya nyasa big bullets kapena kuti kukhala director of supporters mpando uja uli stone mwamadi akuyenela kupeza zochita zina chifukwa mpando uwu ukanikano kuwutenga.

Loweluka lapitali ku club house ya nyasa big bullets kumandala ku Blantyre kunali mkumano wa anthu angapo Ndipo kunali zokambilana zingaposo kumeneko.

Kukumanaku kunachitika loweluka kuyambila nthawi ya 11 mpaka 12 masana masawelo a bullets ndi blue eagles asanaseweledwe ayi.

Ndipo malingana ndi munthu wina emwe anatsina khutu widzman wa mpila soccer zokambilanazo zinagwilizana kuti ku team ya bullets chisankho chisankho director of supporters sichikhalako ayi ndi company ya nyasa ndiyomwe itasankhe munthu emwe akumufuna paudindo umenewu.

Idzi zili chomwechi pangopita sabata imodzi WIDZMAN atalemba nkhani yoti gulu lina likukhoza zozalanda mphavu ya nyasa ngati litasankhidwa kukhala osogolela bullets.

Ndipo company ya nyasa yati lakhazikitsaso maudindo asopano omwe atasankhidweso posachedwapa anthu oti azisogolela bullets nyasa yati pakuyenela kusankhidwa ma chairman kuchokela kuzigawo zonse zamalawi.

Ma chairman akuyenela kukhala anayi kapena kuti 4 Ndipo chair oyamba azisogolela madela ozungulila Blantyre . Ndi ena azisogolela madela monga zomba balaka mangochi liwonde mpaka machinga.

Pomwe chairman wina azisogolela madela monga lilongwe mpaka ku kasungu ndi central region yonse Ndipo omaliza azisogolela mzuzu mpaka karonga ndi nothern region yonse ikuwoneka kuti company ya nyasa apa deal ayiwonela patali ndikuyiponyela kwakuya.

Katswiri wakale wa team ya might tigers komaso bullets Bashir maunde sabata ino Ali paulendo ochoka ku Blantyre ndikulowela ku lilongwe komweno wapatano ganyu wasopano kumeneko

Maunde wapatano shuwa ku team ya civo Ndipo sabata ino akusamuka ku Blantyre ku pita ku lilongwe kukayambano ganyu wake wasopano ku civo.

Polankhula kuchokela ku lilongwe dzulo ndi widzman wa mpila bambo elliya kananji emwe ndi phunzitsi wa team ya civo anati maunde anyamuka week ino kupita ku lilongwe kukakhala ndi amzake kuti akayambeno moyo wasopano.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *