MWATANI KODI A CDEDI?

Malingana ndi chikalata chomwe a bungwe la Center for Democrancy and Economic Development Initiative (CDEDI) yomwewasainira ndi director wawo a Syvester Namiwa atulutsa lelo mmawa chofuna kuti president atule pansi udindo kamba koti walankhula kuti zonse zomwe analonjeza pa nthawi ya kampeni zikhala zovuta kukwaniritsa kamba koti kuli mlili wa Corona.

Malingana ndi bungwe lati a chakwera akuyenera kutula pansi udindo ngati president ndikuti wina okhwima nzeru alamulire nziko lino chifukwa achakwera ndi anzawo ananamiza amalawi pa kampeni nde kuli bwino amalawi apeze mtsogoleri wabwino osati wabkdza ngati achakwera kuti alamulire dziko.

Abungweli ati chakwera ndi boma la Tonse ananamiza anthu kuti Iwo akalowa mu boma azathana ndi matenda acorona koma pano sizikutheka ,malingana ndi bungweli akuti izi ndi zifukwa zokwanira zoti president atulire pansi udindo wawo ndipo dziko lino lisankhenso wina president.

Monga ife a avant Publications tachiona chanzeru kuyankhapo pa zinthu Zina zomwe iwo afotokozazi.

Choyamba ziwani kuti kungolankhula sikuthandiza kanthu koma kuchita, a president anena maganizo awo kuti Zina zomwe analomjeza sizingatheke chifukwa covid19 wafika povuta izi ndi zoona aliyense akuona nde ngati inuyo mungakwanitse bwerani poyera ku mtundu wa amalawi uwuzeni mwina ndikupatsidwa mpata oyendetsa dziko kapena othetsa corona

Achakwera alankhula izi madzulo apa 17 January inu mukufuna pa 19 mupange ma demo Kodi nkhawa zanuzo kapena maganizo anu pa nkhani ya mmene zinthu ziliri mwawapatsa a president ndipo akukanirani? Nanga chithamangira ku ma demo ndi chani?

HRDC ikamapanga ma demo imayamba yakam irana nawo anthu ndikupereka matsiku nde zikalepherekaa anthu amapita ku msewu Kodi inuyo mwachita izi kapena ayi?

Tiuzeni amalawi ngati bungwe, muli naye munthu oti alomwe mmalo mwa chakwera ndi chilima ngati angachoke monga mwakufuna Kwanu?

Kodi dziko lipangisenso chisankho kapena munthu mukumufunayo angolowa?

Pankhani ya ndalama zomwe boma lapereka ku ma lawyers a chakwera ndi chilima munali kuti pomwe boma la DPP limapanga ma appeal osadziwika bwino pa mlandu odziwikiratu kuti aluza? Simumadziwa kuti lizalipire ndi boma? Kapena lero zaipa poti Tonse alliance ndi yomwe yalipira ndalama ku ma lawyers ake omwe?
Tiyeni tiziganiza zinthu zikamachitika osamangolankhula.

Mwati mupanga mademo ndipo mwagwilizana ndi ma vendor kuti atsutsane ndi ganizo lotseka mtsika 5 koloko, pomwe boma la DPP linati litseka mtsika 2 koloko masana bungwe lanulo linali lisanayambe?

Zonsezi tikunenazi bungwe la HRDC linali patsogolo kutsogolera koma pamakhala zokambirana ,Kodi kutseka msika 2 koloko ndi 5 koloko pabwino ndi pati?

Kodi ma vendor aku Lilongwe, mzuzu,kasungu mzimba, dedza, mulanje, nthyolo chitipa mwalankhula nawo kale pa tsiku limodzi lomweli kapena ma vendor aku Blantyre ayimira Tonse amalawi?

Monga ife olemba mkhani tikupempha kuti mubwere poyera ndikunena cholinga chanu pa nkhaniyi kuti amalawi adziwe osati kutimanga mmasamba chifukwa ku ma demo kumakhala gulu Kodi Corona sakafala?

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *