Mwachizolowezi mvula ikamayamba kuchipasula imayamba yaonongako zinthu mderali kamba koti kunadutsa mtsinje wa chipasula m’bali ina
Avantmalawi inamvetsedwa kuti bridge ya chipasula yakokoloka koma atolankhani athu atayendera derali mmawawu apeza kuti Bridge ya Chipasula sinakokoloke.
Avant yapeza kuti madzi anangodzadza chabe pamalopo koma osati kukokoloka.
Komabe ma shop ena ozungulira delari asasuka ndi mphepo ya mphamvu yomwe inabwera dzulo usiku.
Madzi analowanso mmanyumba ena omwe ali mmbali mwa mtsinjewu zomwe zasautsa eni malowo. Chaka ndi chaka boma limapereka thandizo kwa anthu okhudziwa ndi ngozizi kuzungulila delari ndi ma dera ena mu Lilongwe

www.avantmalawi.com
DR MWALE
Share this article