MULANDU WA BAKILI MULUZI WATHETSEDWA

Bwalo la milandu ku blantyre  lero pa 29 April 2023 lathetsa mulandu wa  president woyamba wa ulamuliro wa zipani zambiri a Bakili Muluzi omwe amawaganizira kuti  anazembayitsa ndalama za boma zokwana 1.7 billion kwacha.

Nkhaniyi ikuti amuluzi pamodzi ndi mlembi wawo a Lynes whiskes pa nthawi ya ulamuliro wawo anazembetsa thandizo la ndalamazi zomwe zinachokera ku dziko la Libya kuti zizagwire ntchito yomanga zipatala mu mzinda wa blantyre. Koma ndalamazi zitafika a Muluzi ndi a Lyness anagwilizana kuti ndalamazi zisapite ku boma koma zilowe mthumba mwawo.

Mlandu wa amuluzi unayamba kumvedwa kuchokera pomwe iwo anangochoka m’boma mpaka lero. Pakatipa oyimira a muluzi a Tamando chokhoto anapempha bwalo kuti mulanduwu uthetsedwe popeza ukusowekera chitsogozo komanso umboni okwanira kuchokera ku boma. Koma bwalo la milandu linakana pempholi.

Lero  bwalo la likulu ku Blantyre  lalamula kuti mulanduwu uthetsedwe kamba ka pempho lomwe mkulu owona zofufuzafuza pamilandu  a masauko chipembere anapereka pa 26 may 2023 kuti mulanduwu ungothetsedwa.

Ndizosamvetsetseka kuti mulandu umodzi udzikambidwa pafupifupi zaka 14 koma osapezabe umboni kapena olakwa. Ndalama zomwe zikugwilitsidwa tchito ndi za amalawife, kuchokera pomwe munayambila 2009 mpaka lero mwaononga ndalama zingati? Anafunsa chotera amalawi ochuluka omwe acheza ndi Avant publications  pa nkhaniyi. Amuluzi anamangidwa chaka cha 2009 pa mulanduwi

Katswiri pandale Chimwemwe Tsitsi wati sakugwilizana kwathunthu ndi ganizo la boma lothetsa mlandu okhudza katangale omwe mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Bakili Muluzi amayankha.

A Tsitsi awuza avantmalawi kuti ganizo lomasula Dr Muluzi lili ndi kuthekera kochepsa nkhondo yolimbana ndi katangale.

Bwalori lapanga chiganizochi potsatira pempho la mkulu oyimila boma pa milandu Masauko Chamkakala yemwe anapempha bwalori kuti lithetse mlanduwu.

#DrMwale

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *