MCHEKA AKANIDWA PAKWAWO

Lamulungu pa 4 February 2024, kunali mkumano wa Chipani cha MCP ku mpoto kwa Nsanje kumene kunali mwambo olandira a Esther Mcheka Chilenje kunali zodabwitsa pamene otsatira MCP anakana kulandira mayiyu ndipo anachoka chothawa.

Malipoti akuti a Chilenje amene m’mbuyomu anali a Chipani cha DPP analowa MCP ndipo amayenera kulandiridwa patsikuli ku constituency kutsatira kulandiridwa ndi Pulezidenti wa MCP Dr Lazarus Chakwera ku Mwanza.

Mcheka chilenje athamangitsidwa pakwawo

Mwambo uli mkati a Chilenje anapatsidwa mwayi woti alankhure ndi anthu , iwo anayamba kuyamikira utsogoleri wa Dr Lazarus McCarthy Chakwera. Mkati mwa kulankhula kwawo iwo anati ndikhumbo lawo kuzayima ngati phungu ku Mmawa kwa dera la Machinjiri ku Blantyre, koma ataunikira zoti kumpoto kwa Nsanje North sikukubwera zitukuko iwo aganiza zozapikisana ndi a Enock Chizuzu pa by elections.

Atangolankhula izi kunali chipwilikiti chachikulu pamene anthu anayamba kuwowoza komanso kugenda ku nsanja komwe anayima a Chilenje.

Pakuona kuti zavuta a Chilenje anasiya kulankhula ndi kutulukira panja pozera khomo la kuseri kwa holoyo ulendo kukakwera galimoto kumapita.

Kulankhula kwa Mcheka Chilenje asanathamangitsidwe ndi anthu

Ngakhale zili chomwechi chiyembekezo chachikulu chilipo choti a Chilenje azayimabe ngati Mphungu wa MCP ku machinjiri dera la Blantyre.

Zambiri tsatani Avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *