MANKHWALA AMBIRI ATHA MPHAMVU

Pamene mzipatala zambiri mankhwala akhala akusowa oti azithandizira anthu odwala zadziwika tsopano kuti mankhwala ambiri a ndalama zoposera 2 billion awonongeka ku malo osungira mankhwala.

Kuonongekaku sikuti kwadza kamba kosasamala ayi koma kusawagwilitsa ntchito mankhwala ndipo nthawi yomwe anawaika kuti izakhale atagwira ntchito yadutsa.

Mdziko muno anthu akhala akudandaula kuti mankhwala mzipatala mulibe ,ndipo ambiri amauzidwa kuti akagule kuma famase koma lero amalawi akhala odabwa kumva  kuti mankhwala awonongeka komwe amasungidwa.  Kodi amawasunga kuti ndi achani? Kodi amafuna kuzapatsa odwala ake ati? Kapena pogulapo amagulira kuti ndi ntchito yanji?
Mafunsowa ndi omwe amalawi ambiri akufunsa kamba kokhumudwa ndi nkhaniyi.

Izi zapatsa chidwi amalawi ndipo azifunsa mafunso oti ogwira ntchito mu medical store samaona date lomwe mankhwalawo azathere mphamvu? Kodi nduna ya zaumoyo simayendera malowa? Chokhumudwitsa kwambiri ndichakuti palibenso kuchitira mwina mankhwalawa kuyenera kuotchedwa basi ,komwe ndi kuononga misonkho ya amalawi omwe akuvutikanso Kufuna mankhwala omwewo pokagula okha.

Pakadali pano boma zikuyenera kupeza  ndalama zochuluka zoti agule mankhwala oti azakwanire mzipatala zonse mdziko muno

www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *