MAKOLO AKUDANDAULA NDI MKHALIDWE WA APHUNZISI APA FACE SECONDARY KU ZALEWA

olemba Dr mwale

Boma la la Germany linapereka nthandizo la zamaphunziro ku boma la malawi powamangira sukulu ya ulelere yomwe ana ovutikitsika azipitako ulele, inde iyi ndi sukulu ya secondary.

M’mbuyomu anawa amaphunzira bwino bwino kopanda kulipira kapena kuvutika mwa njira ina, koma nkhani tabwera naye pano lero ndi yakuti a head apa sukuluyi omwe ndi a Mr Chitekwe tsopano atenga sukuluyi ngati yawo.

Chomwe chikuchitika pasukulupa ndi chakuti thandizo lonse la sukuluyi limapereka ndi boma la Germany zomwe zikuthandauza kuti mwana sakuyenera kulipira kalikonse koma ahead apa face anayamba kuuza anawa kuti azilipira ma 900 aliyense pa teremu zomwe zikudabwitsa makolo kuti ndalamayo ikupita kuti komanso ikugwira ntchito yanji? Makolo akati afunse amawaopseza kuti akapitiliza ana awo achotsedwa sukulu. Avant publications yapeza kuti ana akangolakwitsa pang’ono amawatulutsa nkalatsi kuti akalime ndime ya mizere 30 tangoganizani. Kulima sichibalo chapa sukulu

Mwana wina anapezeka ndi mimba pa sukulupa pa nthawi ya covid19 koma ahead amenewa anawapasa sasi anawa ya masabata atatu pomwe kutasala mwezi umodzi kuti alembe mayeso.atabwera ku sasi mwanayo anawapatsidwa chibalo pamodzi ndi anzake choti akumbe toilet. Izi zikusiyana ndi zomwe boma limalankhula kuti mwana yemwe ali ndi mimba aziloledwa kupita ku sukulu. Chodandaulitsa kwambiri ndi chakuti ahediwa anafika powapasanso chibalo makolo a anawa kuti akalime mmunda wapa sukulupo ndipo kupanda kutero anawo achitsedwa pa sukulu. Komanso amatero?

Makolowa akuti a hedi ndi omwe akuchita khalidwe lopusali. Ndalama zomwe anawa akulipira akuti zimalowa mthumba mwa ahedi ndipo sikugwira ntchito yaku khichini pakuti boma la German limapanga chilichonse.

Ana a sukulu anapanga sitalaka kuti athane ndi mchitidwe wa head amenewa .

Nawo makolo akwiya ndi khalidwe la hedi ameneyu ndipo akufuna kuti hediyi ameneyu achoke pa sukulupa ndipo ku zalewa achokeko chifukwa ubale wake ndi anthu a mudzi suli bwino nde kuopa kupewa zambiri anthuwa akuti mkuluyi achoke. Chifukwa choti afika pomawatchula anawa kuti akapolo awo.

Avant publications italankhula ndi makolo akuderali akuti nawo zawatopetsa ndipo akufuna a unduna owona zamaphunziro a Agness nyalonje kuti abwere kuzathandiza kuthana ndi mavutowa chifukwa muvi oyang’anira suchedwa kulowa mmaso.

Nawo a unduna owona za ufulu wa ana abwere pa sukuluyi kuti azathandize kuona mavuto omwe alipowa.

Face sekondale ili pa zalewa ndipo ili pa mtunda wa malipande okwana 500 kuchoka pa nsewu.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *