Olemba Dr mwale
Avant publications ndi nyumba yofalitsa nkhani yomwe imadziwa kuti monga munthu sungakwanitse kumvera nkhani zonse kamba kotanganidwa ndi zinthu Zina, ichi ndichifukwa chake timakubweretserani nkhani zathu zikulu zikulu zomwe zinachitika msabata yongothayi. Tiyambe motere!
Boma la Tonse likhazikitsa tsiku lochotsa zinyalala
President wadziko lino komanso wachiwiri wake msabatayi anali ku chigawo Cha ku kumpoto komwe anakhazikitsa tsiku loti amalawi azisesa m’mizinda komanso m’misika ndi malo ozungulira kuti zinyalala zomwe zikungotayidwa paliponse zichoke. Mtsogoleriyu wati ntchitoyi izichitika Malawi yonse ndipo izichitika lachisanu lachiwiri pa mwezi ulionse. Malingana ndi Avant mtsogoleriyu sananene kuti tsikulo lizikhala la tchuti kapena ayi. Pakadali pano ntchitoyi yatsegulidwa ndi nduna zosiyanasiyana m’maboma onse dziko muno, komwe ma reporter anthu anakwanitsa kupita kukatola zithunzi.
President Chakwera anapita ku South Africa.
President wa dziko lino a DR Chakwera anapita mu dziko la South Africa komwe amakakumana ndi president Cyril Ramaphosa ndipo mwa Zina kumeneko Chakwera wapempha president Ramaphosa kuti aganizire zopereka zikalata zololeza amalawi kuti azigwira ntchito m’dzikolo mwaufulu, Chakwera wati amalawi akumapatsidwa mwezi umodzi oyenda mwaufulu kudzikolo pomwe anthu amaiko ena akumapatsidwa miyezi itatu zomwe sizabwino konse kwa amalawi ndipo president Ramaphosa wati wamva pemphori.
Mlandu wa zisankho ku nsanje kuli zii
Amalawi akudikirabe ndi chidwi kuti awone m’mene Mulandu wachisankho omwe a Enock chizuzu anasumira MEC komanso a Ester mcheka chilenje kamba koti masankho akumeneko sanayendwe bwino. Mlanduwu bwalo lamilandu linamaliza kuumva koma pano pafupifupi miyezi itatu yadutsa ma jaji sakupereka tsiku lachigamulo Kodi chavuta ndi chani? Mtundu wa amalawi ukudikira. Sitinayiwalile!
UTM sinapeze mpando pachisankho Cha chibwereza
Pa 10 november 2020 m’dziko muno munachitika chisankho Cha chibwereza ndipo chinachitika mma boma atatu omwe ndi karonga ,Lilongwe komanso chikwawa. Koma ku karonga ndi ku Lilongwe inapambana ndi MCP pamene ku chikwawa inawina ndi UDF. Izi zazetsa nkhawa kwa masapota achipani cha UTM poti Iwo sanapeze mpando zomwe zikuthandauza kuti MCP ikuchulukitsa aphungu mu nyumba ya malamulo kuposa UTM. komabe chosangalatsa ndi chakuti zipani ziwirizi zili pa mgwilizano ndipo zonse akuchitira limodzi. Izi zisabweretse kugawanikana, ayi, kumbukirani komwe mwachoka.
MEC ichedwetsa kulengeza opambana pa chisankho Cha chibwereza.
Avant publications inapeza kuti MEC inalephera kulengeza mwachangu zotsatira za chisankho chachibwereza kamba koti ma komishonala awo awiri omwe ndi amathanga komanso a kunje anakana kukhala nawo pazisankhozi kamba koti sakulandila nawo ndalama za makomishonala poti mtsogoleri wa dziko lino akukana kuwapatsa zikalata zowavomereza pa udindowu.
A Mpinganjira anaonekera ku bwalo la milandu.
Mponda matiki yemwe amafuna kugula ma jaji kuti aweruze mlandu mokomera chipani Cha DPP anaonekera ku bwalo la milandu pomwe mboni yoyamba imamaliza kuperekera umboni wake. Kunali kukana ma loya a Mpinganjira kuti mlandu uyambe kamba koti jaji amamva mkanduwu kuzera pa video conference koma izi sizinaphure kanthu kamba koti bwalo linakana pempholi.
Ngakhale zili Chomwechi, kafukufuku akuonetsa kuti odandaula Ali ndi umboni ochuluka umene ukusonyeza kuti a mpinganjira ngati sachenjera zinthu siziwathera bwino, pamulanduwu.
Chisale akana mlandu wa setifiketi
Yemwe anali wachitetezo wa president wakale wa dziko lino a Normani
chisale anakaonekera mu bwalo la milandu dzana komwe amakayankha mulandu wawo ogwiritsa ntchito setifiketi ya fomu 4 ya munthu wina ndipo anachita izi zaka 26 zapitazo. iwo anakasinthitsa dzina ku maneb. Achisale anaukana mulanduwu ndipo boma likuti Lili ndi mboni zokwa zisanu ndi zitatu pa nkhaniyi zomwe zizayambe kuperekera umboni pa 30 November. Achisale akuyembekezeka kulowanso mu khoti pa 23 pomweakuzayankhanso mulandu wina.
Maneb iyimitsa pa ntchito anthu ena
Bungwe loona za mayeso mdziko muno la maneb laimitsa pa ntchito akulu akulu a bungweli kamba ka zomwe zinachitika potulutsa mayeso asanalembedwe. Mchikalata chawo zaonetsa kuti anthu oposera asanu ndi awiri anaimitsidwa pa ntchito kuti afufuzidwe. Izi zadza kamba ka zomwe president Chakwera analamula kamba kukhumudwa ndi mchitidwe obera mayeso omwe wapangitsa kuti chaka Cha 2020 mayeso a MSCE alephereke.
Ngongole ya NEEF(MARDEF)
Malingana ndi boma la Tonse aliyense yemwe akufuna ngongole apange magulu ndipo akapereke ku bungwe loona za ngongoleyi kudzera mwa adindo monga a khansala ndipo kumeneko akawauza zochita
Bushiri athawa ku South Africa.
Mneneri wa mpingo wa ECG wathawa mdziko la South Africa komwe ali ndi mlandu omwe akumuganizira kuti anazembetsa ndalama. Bushiri anamuletsa kutuluka mdziko la South Africa mpaka mlunduwu utatha koma loweluka lapitali anthu anazizimuka kumva kuti mneneri bushiri Ali mdziko muno kamba koti moyo wake kumeneko unali pa chiopsezo. Kodi bushiri wayenda bwanji? Wabwera pa ndege nanga ndegeyo yanyamuka bwanji mdzikolo? Apatu Pali nkhani.
Feteleza otchipa abweretsa Mavuto.
Avanti inalandira ma report komanso inazionera yokha pamene makolo athu akugona ku Farmers world komanso Chipiku kudikira kugula Feteleza otchipa.
Ngakhale zili chonchi boma sili kulankhulana kuti vuto ndichani komanso anthuwa athandizidwa motani muthawi ya Mvula ngati imeneyi. Kodi tiziti network imavuta panthawi yogula feteleza Basi? Bwanji network sivuta nthawi yogawa ma ballot box komanso kuvota?
Ma Bungwe a Admarc, Maneb komanso MRA Ayimitsa ogwira ntchito
Pamene a Malawi takhala tikudandaula za zinyengo mu ma Bungwe a boma ngati MRA komanso kusokonekera kwa Mayeso a MANEB.
Sabatayi tawona mabwana ena akulandirazibaluwa kuti apiteku Ntchuti chokakamiza ndi kusankha ena otiagwire ntchito mmalo mwawo. Ngakhale izi zili Chonchi, koma anyamata omenyerera ufulu a HRDC awonetsa kusakhutira ndi kuchedwa kwa boma la Tonse alliance pakupanga ziganizo zawo.
Flames ndi Scorches akugonja mumasewero awo*
Timu ya dziko lino ya mpira wa myendo osewera ake kukhala amuna yagonja masewero ake oyamba mpikisano wa AFCON pomwe yinakunamuna ndi timu ya Burkina Mzinda wa Ouagadungou, timu ya dziko lina yogonja 3-1 izi zachitikaso ku timu ya mpira wa myendo koma osewera ake kukhala asikana omwe agonjaso ndi timu ya South Africa 6-1 mpikisano wa COSAFA
Werengani zambiri pa www.avantmalawi.com
DR MWALE