KUNALI CHI MDIMA KU NYUMBA YA MALAMULO

Mmawawu kunali mdima ku Nyumba ya Malamulo kupangitsa a Speaker kulamula kuti aphungu apite kopumila.

Izi zadzidzimutsa anthu omwe afunsa boma kuti afotokoze komanso akonze mavuto a Magetsi ku Parliament.

Kuzimazima kwa Magetsi kwachitika motsagana katatu kuchoka mu 2020

Zimene zachititsa kuti magetsi athime mmawawu sizikudziwika, ngakhale pali kukayikira kuti pali vuto ndi kalumikizidwe ka Magetsiwa mu denga lomwe limatchedwa ceiling.

Amphunguwa atazikakamiza kupitilira ndizokambirana kumasana kunalinso fungo lodabwitsa limene linapangitsa ena mwa aphungunguwo kutuluka mu Nyumbayi.

Funguli limamveka ngati zithu zikuphysa ndipo Sipikara wa Nyumbayi analamula kuti apumile zokambilana zawo.

Titalankhula ndi Tsogoleri wa Nyumbayi, Hon Richard Chimwendo anati iwo Ali okhudzika kwambiri ndipo ayitana katswiri owona zamagetsi kuti awone vuto lomwe lilipo komanso akonze vutolo

Kuzima kwa magetsi kwabwera pamene kuli load shedding mdziko muno, komabe anthu ambiri azifunsa mafunso omwe mayankho ake sakupezeka monga kuti kodi nyumbayi kulibe ma geneleta?

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *