KUGWETSA MULATHO WA LILONGWE

Mlatho wa Lilongwe Watsekedwa Lero pa 16 November 2023 pokonzekera kugwetsa kwa mlathowu.

Mmawa uno mlathowu watsekedwa ndipo magalimoto akudutsa ku manja kwa mlathowu tikamachoka ku Area 3 kudzera ku ma office a Escom. Anthu oyenda pansi nawo akudutsa ku Manzere kwa Old Town kumene kwamangidwa mlatho wa ung’ono oyende pansi.

Kuli Anthu ochuluka amene akutsimikiza za mmene mlathowu ugwetsedwere pokonzekera kumanga mlatho wa tsopano.

Mlathowu unamangidwa nthawi ya Dr Hastings Kamuzu Banda ndipo wakhala zaka zochuluka zedi uli chilimbire kotero anthu ochuluka ali ndi Chidwi ngati boma likwanitse kumanga mlatho olimba pamalopo oti uzakhaleso zaka zochuluka ku tsogoloku.

Zambiri tsatani Avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *