Bwalo lomwe likumva mlandu wa bambo Vincent Dzimadzi womwenso amadziwika ndi dzina loti a Gabi lakana kupereka belo lero kuntcheu.
Yemwe akumva mlanduwu magistrate J Nkono wakana kupereka belo ponena kuti bambo Vincent Dzimadzi akhonza kuthawa ku Malawi kuno poti iwowo amakhala kumalire adziko lino ndi Mozambique.
Bamboyu anamangidwa sabata latha poganizilidwa mlandu womenya mwana mwankhanza yemwe akuti amawabera mbatata.
Avanti linali ndi chidwi ndi khwimbi la anthu omwe anakhamukira ku khothi. Mlanduwu wayimitsidwa ndipo udzapitiliraso pa 3 December 2021.
Share this article