JOYCE BANDA AKAIMIRA CHAKWERA KU MALILO A KIBAKI

Pomwe president wa dziko ali otanganidwa ndi ntchito zina, mphamvu zinapatsidwa kwaiye kutumiza anthu ena kukamuimira pa ntchito zomwe akanatha kupita yekha.

President wa dziko lino wasankha mtsogoleri Wakale wachizimayi wa dziko lino mayi Joyce Banda kuti akakhale nawo pa mwambo oyika mmanda president wakale waku Kenya a Emiliano Mwai Kibaki omwe anamwalira pa 21 April 2022 ndipo azaikidwa mmanda pa 30 April 2022.

A kibaki anabadwa pa 15 november 1931 ndipo amwalira ali ndi zaka 90. Ndipo anasiya ana anayi.
A Kibaki anakhala president wachitatu wa dziko la Kenya ndipo analammulira dzikolo kuchokera 2003 mpaka 2013 ndipo analamulira limodzi ndi Joyce Banda. Pa ulendo wake obwera kuno a Kibaki anatsekulira limodzi msewu wa by pass ku Lilongwe ndi mayi Joyce banda.

Abanda ati ndi osangalala kuti akhala nawo pa mwambo wa president wakaleyu. Iwo ayamika mtsogoleri wa dziko linoyu powatuma. Achakwera anatumanso a muluzi kupita ku zambia kukakhalanso pa mwambo wa maliro a president opuma kumeneko.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *