DPP YASINTHA MASIKU OCHITITSA BLUE PARADE

Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) chasintha tsiku lomwe chipanichi chinakonza kuyenda ndi mdipiti wamagalimoto pachingerezi ‘blue convoy parade’ ku Machinga ndipo mmalo mwa lero la Mulungu mdipitiwu udzachitika mawa, lolemba.

Polankhulapo pazakusinthaku, Gavanala wachipani cha DPP chigawo chakummawa a Emran Ntenje ati izi zachitika kamba ka zovuta zina.

A Ntenje ati mwazina pamdipitiwu Iwo adzalimbikitsa otsatira chipanichi kukalembetsa mwaunyinji mkaundula wa ziphatso zaunzika kuti adzakhale ndikuthekera koponya nawo mavoti achaka chamawa.

Mdipiti ngati womwewu unakonzedwanso mu mzinda wa Lilongwe pa 24 February koma anthu ena omwe mpaka pano sakudziwika anachitira Chiwembu ndikuvulaza otsatira chipani Cha DPP.

(Dumisani Mwambazi-Mchinji)

avantmalawi.com
03/03/2024

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *