CHIHANA NDI WA BODZA

Olemba Dr Mwale

Phungu wa wadera la kumpoto kwa boma la mzimba a yeremiah chihana awonekera ng’amba pomwe alephera kupereka umboni wa nkhani yomwe iwo anauza nyumba ya malamulo kuti nduna za boma la Tonse zikulandira ziphuphu kuchokera ku anthu akunja.

Koma atapanikizika munyumbayi lero pa 16 September chihana wabwera poyera ndikunena kuti iye Amanama ndipo alibe umboni pa nkhaniyi,

Nthawi zambiri achihana amakonda kulankhuka zinthu zomwe zimaoneka ngati zoona koma pamapeto pake sizikumankhala ndi umboni. Posachedwapa chihana anauzanso anthh kuti ali ndi umboni pa za anthu omwe akumangidwawa kuti milandu yawo ikubwera kamba ka ndale   koma palibe chomwe ananena chanzeru.

Amalawi tsopano maso awo ali pa sipikala wa nyumba ya malamulo mayi Catherine Gotani Hara kuti apereka chilango chotani kwa a chihana monga mwa lonjezo lawo.

Aphungu akunyumba ya malamulo komwe muliko dziwani kuti anthu amadalira inu komwe mwachokera nde mukamapanga masanje ngati awa dziko simuyendetsa bwino.
Avant publications ikutsindika pano kuti Yeremiah Chihana ndi wabodza ndipo amangonamiza anthu mu parliament.

Tiyamikire www.avantmalawi.com otsogolera nyumbayi ku mbali ya boma a Richard Chimwendo Banda pobwera poyera kuti achihana apereke umboni komanso a president athu powauza achihana kuti awalodzere komwe kuli ndalama zomwe iwo amanena.

Funso kumati aford ili nawo mu Tonse alliance Kodi achihana  omwe ndi phungu yekhayo wa afford munyumbayi akuchita izi chifukwa chani?

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *