olemba Dr Mwale
Anthu akumwanza tsopono chimwemwe chili nsaya kamba koti boma tsopano lavomereza pempho loti limange bwalo la zamasewero ku mwanza.
Masiku apitawo phungu yemwe akufuna kuzaimira chipani cha UTM ku chigawo chapati mu boma la mwanza olemekezeka a Felix Njawala adachititsa msonkhano ndipo mmawu awo, iwo adapempha Boma kuti limange Malo osewerera mpira mu Bomali, ndipo iwo adauza boma kuti ngati Samanga bwaloli iwo azamema anthu kukachita zionetsero Kuboda ya boma la mwanza ndicholinga chokakamiza boma kuti lime pempho Lawo ndikukwanilitsa zofuna za anthu a mderalo.
Mawu a a Njawala sadagwe pa mwala koma pa nthaka yabwino kamba koti boma lavomereza pempho lawo ndikuika ndalama zokwana 1 billion kwacha kuti anthu ayambe kumanga bwaloli.
Mu nyuzi pepala ya lero Boma likuitana akadaulo oziwa kumanga mabwalo azamasewero kuti alembere za ntchitoyi.
Mawu awo a Njawala ati ndiokondwa kwambiri kuti boma lamva pempho lawo ponena kuti izi ndi zomwe amayembekezera kuti boma lizichita anthu akapempha. Ndipo iwo ati akalowa mu boma ngati phungu wa UTM mu 2025 azabweretsa zitukuko zosiyana siyana kudera lawo kamba koti ndi khumbo lawo kutulula dera lawo ku mwanza. “Anthu ena akhala pa mpandowu zaka zochuluka koma samaganizira za kuthandiza achinyamata komanso kutukula masewero a mpira mubomali. bwaloli limayenera kumangidwa mu chaka cha 2020, ndalama zinatuluka kale ndipo omanga anapezeka koma mpaka pano kuli zii. Izi ndi zomwe zandipangitsa kuti ndilankhulie Mwanza yense osati dera lokhalo lomwe ndizaimire” atero a Njawala.
Atafunsidwa kuti boma lakuyankhani changu pempho lanu mwina potengera kuti muli nawo mu boma la Tonse? Iwo sanabitse chichewa ponena kuti sizoona kuti ayankhaidwa changu kamba koti ali nawo mu Tonse alliance koma kuti bomalo lawona chidwi chomwe iwo ali nacho komanso kufunika kwa bwaloli kwa anthu akumwanza. Zikanati zitengere chipani bwezi aphungu alipowo atamanga kale pansi pa ulamuliro wa zipani zawo zaka zonse zomwe akhala akulamula” atero a Njawala.
pamapeto pake Iwo apempha achinyamata komanso anthu onse okhala mudera lomwe iwo azayimire kuti azavotere iwo ngati phungu wa UTM kuti zitukuko zambiri zizapitiire.
Pakadali pano phungu wa derali ndi olemekeza Nicholus Dausi a chipani cha DPP. Ndipo ndi omwe azapikisane kwambiri ndi a Felix Njawala achipani cha UTM omwenso ndi mneneri wachipanichi pakadali pano.

www.avantmalawi.com
DR MWALE