BALABA ATHETSA VUTO LA MADZI KU NYAMBADWE

Wachiwiri kwa Meya wa mzinda wa Blantyre yemwenso ndi nkhansala wa chipani cha UTM ku Nyambadwe ward lero wakatsekulira malo otungira madzi atatu muderali ndicholinga chofuna kuthana ndi vuto la kusowa kwa madzi.

Olemekezeka meya Funny Balaba omwe ndi mmodzi mwa oyang’anira a chinyamata mu chipani cha UTM lero ku mmawaku amatsegulira malo otungira madzi akwana atatu omwe tsopano aperekedwa kwa anthu a ku nyambadwe, malingana ndi a balaba iwo ati anthu aku Blantyre makamaka ku nyambadwe akhala akuvutika kwa nthawi yaitala kuti apeze malo abwino otunga madzi,izi zinawapangitsa iwo kuti apeze thandizo loti madzi a ukhondo abwere mdera lawo.

councillor Balaba

Abalaba ati ichi ndi chiyambi chabe ndipo akufuna kuti dera lawo lonse lisazavutikenso madzi mpaka kalekale.

A Balaba apempha anthu onse omwe azungulira derali kuti asamale malowo komanso madziwo kamba koti ndi moyo wawo. Iwo apemphanso mafumu kuti awonetsetse kuti akupereka chitetezo chokwanira ku malo otungira madziwa ponena kuti chitukuko chimayamba ndi madzi. Posachedwapa vuto la madzi likhala mbiri ya dzanala mdera la nyambadwe watero balaba.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *