- Olemba Dr MWALE
Ma dalaivala a ma minbus mu mzinda wa Blantyre lero anyanyala ntchito zawo kamba ka ganizo la boma kuzera mu bungwe la Mera lokweza mafuta a galimoto.
Anthuwa anagwilizana dzulo kuti kuyambira lero iwo ayamba kunyanyala ntchito mpaka boma litamva ndikuyankha madandu awo.

Avant publication itamva za nkhaniyi inathamangira muzinda wa Blantyre komwe yazionera yokha ndi maso, tinakwanitsa kulankhula ndi mmodzi mwa anthu omwe amayenda wapansi kuchokera ku bangwe kupita mtawuni, awa ndi Mr chagunda iwo amagwira ntchito ku GM Plastic ndipo akuti akakamizidwa kuyenda wapansi kuchokera ku Bangwe kufika mu limbi zomwe zawapangitsa kuti akafike mochedwa ku ntchito, iwo akuti boma likuyenera kumva madandu a anthu mwachangu kuti mavutowa athetsedwe.
Mayi wina yemwe amachokera ku mbayani koma wati tisamutchure dzina wati anthu anazolowera kukwera minubus pa maulendo awo nde kukakamizidwa kuyenda wa pansi kamba ka kukwera kwa mafuta sichinthu choyenera, nafe tinavotera boma la Tonse nde tikamadandaula kumatimvera ,mitenngo ya mafuta itsike, watero mzimayiyu.

Mavuto oyenda pansiwa achitikanso ku namiwawa, chilomoni ndi Madera ena ambiri mzindawu.
Apolice apa kudya station anakwanitsa kuthamangitsa ma dalaivala omwe anatseka msewu koma atangkchokapo pa malopo madalaivalawa anabweranso ndikutseka msewu.
Chomwe anthuwa akufuna ndi chakuti boma litsitse mtendo wa mafuta kapena kuti awalore kuti azitenga anthu atatu atatu pa mpando osati awiri kuti nawo azipeza phindu.

Mademowa a chitika mu mzinda wa Blantyre wokha, Kodi ku mzuzu ndi ku lilongwe anthu mwasangalala nazo zokweza mitengo yamafutazi?
www.avantmalawi.com