Atoti Manje watisiya imfa yodzidzimutsa

Zatsimikizika kuti oyimbayu amene dzina lake leni leni ndi Elias Missi Wamwalira pa Chipatala Cha Livingstonia Ku Khondowe (Rumphi) atangomaliza kuyimba ku unilia.

Mmodzi mwa anamwino a zachipatala cha Rumphi watsimikiza kuti oyimbayu anafika ali chikomokere chifukwa amadandaula mthupi komanso kumva kutentha.

Mu zikalalata zina za kuchipatala zikuti oyimbayu anali ndi vuto m’mapapo

Mlembi wa sukulu ya ukachenjede ya Livingstonia Rev John Gondwe watsimikiza zaimfa ya oyimbayu, amene watisiya usiku wapa pa 7 October atangomaliza kuimba pamphwando lamayimbidwe lomwe linakonzedwa ku sukulu ya ukachenjede ya Livingstonia ku laws campus ku Khondowe m’boma la Rumphi.

Pakadali pano thupi la malemu Atothi Manje akulitengera kuchipatala cha Mzuzu Central kuti akalipime pamenenso akudikira achibale.

Oyimbayu ayikidwa mmanda pa 9 October kwawo ku Mangochi. Oyimbayu anabadwa chaka cha 1989 wasiya ana anayi ndi mkazi mmodzi

Tionere nyimbo imene oyimbayu anayimba asanamwalire

AVANT Publications

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *